September 2-8
AHEBERI 7-8
Nyimbo Na. 16 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Wansembe Mpaka Muyaya Monga mwa Unsembe wa Melekizedeki”: (10 min.)
Aheb. 7:1, 2—Melekizedeki yemwe anali mfumu komanso wansembe anakumana ndi Abulahamu n’kumudalitsa (it-2 366)
Aheb. 7:3—Melekizedeki analibe “mzere wa mibadwo ya makolo” ndipo anakhala “wansembe kwamuyaya” (it-2 367 ¶4)
Aheb. 7:17—Yesu ndi “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki” (it-2 366)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Aheb. 8:3—Kodi pali kusiyana kotani pakati pa mphatso ndi nsembe zomwe anthu ankapereka malinga ndi Chilamulo cha Mose? (w00 8/15 14 ¶11)
Aheb. 8:13—Kodi pangano la Chilamulo linakhala bwanji “lotha ntchito” m’nthawi ya Yeremiya? (it-1 523 ¶5)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Aheb. 7:1-17 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kugwiritsa Ntchito Bwino Zinthu Zooneka, kenako kambiranani phunziro 9 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) it-1 524 ¶3-5—Mutu: Kodi Pangano Latsopano N’chiyani? (th phunziro 7)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Gulu Lathu Lachita: (15 min.) Onerani vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya September. Limbikitsani abale ndi alongo kuti ngati angathe akaone malo ku ofesi ya nthambi kapena kulikulu lathu lapadziko lonse.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 49
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 70 ndi Pemphero