Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr19 September tsamba 1-7
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
  • Timitu
  • SEPTEMBER 2-8
  • SEPTEMBER 9-15
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
  • SEPTEMBER 16-22
  • SEPTEMBER 23-29
  • SEPTEMBER 30–​OCTOBER 6
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
mwbr19 September tsamba 1-7

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

SEPTEMBER 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 7-8

“Wansembe Mpaka Muyaya Monga mwa Unsembe wa Melekizedeki”

it-2 366

Melekizedeki

Melekizedeki anali mfumu ya mzinda wakale wotchedwa Salemu komanso anali “wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba,” Yehova. (Gen. 14:18, 22) Iye ndi wansembe woyamba kutchulidwa m’Malemba ndipo anakhala paudindowu nthawi inayake chisanafike chaka cha 1933 B.C.E. Ndiye popeza anali mfumu ya mzinda wa Salemu, dzina limene limatanthauza “Mtendere,” Paulo anatchula Melekizedeki kuti anali “Mfumu Yamtendere” ndipo potengera tanthauzo la dzina lake, anamutchula kuti “Mfumu Yachilungamo.” (Aheb. 7:1, 2) Zikuoneka kuti mzinda wakale wa Salemu unali pakati penipeni pa mzinda womwe unadzayamba kudziwika kuti Yerusalemu. Ichi n’chifukwa chake mbali ina ya dzinali inaphatikizidwa ku dzina lakuti Yerusalemu, yemwe nthawi zina ankatchedwanso kuti “Salemu.”​—Sal. 76:2.

Pa nthawi ina Abulamu (Abulahamu) anagonjetsa Kedorelaomere limodzi ndi mafumu amene anali naye ndipo kenako anatsikira ku Chigwa cha Save, kapena kuti “Chigwa cha Mfumu.” Kumeneko Melekizedeki “anabweretsa mkate ndi vinyo” ndipo anadalitsa Abulamu n’kunena kuti: “Mulungu Wam’mwambamwamba adalitse Abulamu, Iye amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo adalitsike Mulungu Wam’mwambamwamba, amene wapereka okupondereza m’manja mwako!” Zitatero Abulamu, anamupatsa “chakhumi” kuchokera pa “zinthu zabwino kwambiri zimene anafunkha” atagonjetsa magulu ankhondo a mafumu aja.​—Gen. 14:17-20; Aheb. 7:4.

it-2 367 ¶4

Melekizedeki

Kodi n’zoona kuti tsiku limene Melekizedeki ‘anabadwa komanso kumwalira silikudziwika’?

Paulo anatchula mfundo yochititsa chidwi kwambiri ponena za Melekizedeki. Iye anati: “Popeza kuti analibe bambo, analibe mayi, analibe mzere wa mibadwo ya makolo ndipo tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalira silikudziwika, koma anamuchititsa kuti afanane ndi Mwana wa Mulungu, iye ndi wansembe kwamuyaya.” (Aheb. 7:3) Mofanana ndi anthu onse, Melekizedeki anachita kubadwa ndipo kenako anamwalira. Komabe, mayina a bambo ndi mayi ake sadziwika. Komanso palibe amadziwa mibadwo ya makolo ake ndipo Malemba samanena chilichonse chokhudza tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalira. Choncho tinganenedi kuti Melekizedeki anali woyenera kuimira Yesu Khristu, yemwe ndi wansembe mpaka muyaya. Melekizedeki sanalandire udindo wake monga wansembe kuchokera kwa munthu wina komanso palibe amene anamulowa m’malo. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limasonyezanso kuti Khristu sanachite kulandira udindowu kuchokera kwa munthu wina ndipo palibe amene adzamulowe m’malo monga mkulu wa ansembe. Komanso, ngakhale kuti Yesu anabadwira mumtundu wa Yuda, mumzera wachifumu wa Davide, makolo ake sanali m’banja la ansembe komanso sizinkachitikachitika kuti munthu akhale mfumu ndiponso wansembe pa nthawi imodzi. Koma zimenezi zinachitika chifukwa cha zomwe Yehova anamulonjeza.

it-2 366

Melekizedeki

Unsembe wa Khristu Unali Wapadera. Pali ulosi wina wochititsa chidwi womwe umanena za Mesiya. Ulosi umenewu umasonyeza kuti Yehova analumbira kwa “Ambuye” wake wa Davide kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale, monga mwa unsembe wa Melekizedeki!” (Sal. 110:1, 4) Ulosiwu unachititsa kuti Aheberi aziyembekezera kuti Mesiya wolonjezedwayo adzakhala wansembe komanso mfumu pa nthawi imodzi. Polemba kalata yake yopita kwa Aheberi, mtumwi Paulo anawatsimikizira kuti ulosi uja unkanena za Yesu amene “wakhala mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”​—Aheb. 6:20; 5:10.

it-1 1113 ¶4-5

Unsembe wa Melekizedeki. Melekizedeki ndi wansembe woyamba kutchulidwa m’Baibulo. Iye anali “wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba” komanso anali mfumu ya mzinda wotchedwa Salemu (Yerusalemu). Abulahamu anakumana ndi mfumuyi pamene ankachokera kogonjetsa mafumu atatu omwe anachita mgwirizano ndi Kedorelaomere mfumu ya ku Elamu. Abulahamu anasonyeza kuti anazindikira kuti Melekizedeki anali wansembe wa Mulungu pomupatsa chakhumi pa zinthu zimene anafunkha atagonjetsa adani ake komanso polandira madalitso amene Melekizedeki anamupatsa. Malemba samanena chilichonse chokhudza tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalira. Melekizedeki sanalandire udindo wake monga wansembe kuchokera kwa munthu wina komanso palibe amene anamulowa m’malo.​—Gen. 14:17-24.

Unsembe wa Yesu Khristu. Buku la m’Baibulo la Aheberi limanena kuti Yesu Khristu, kungochokera pamene anaukitsidwa n’kupita kumwamba, anakhala “mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.” (Aheb. 6:20; 7:17, 21) Pofuna kusonyeza kuti unsembe wa Khristu ndi wapamwamba kwambiri kuposa wa ansembe a m’banja la Aroni, wolemba buku la Aheberi ananena kuti Melekizedeki anali mfumu komanso wansembe pa nthawi imodzi ndipo anapatsidwa udindowu ndi Mulungu Wam’mwambamwamba, komanso kuti sanachite kulandira udindowu kuchokera kwa makolo ake. Mofanana ndi zimenezi, Khristu Yesu sanali wa m’fuko la Levi, koma fuko la Yuda ndipo anali wochokera mumzera wa Davide. Choncho tinganene kuti sanachite kulandira udindowu kuchokera kwa Aroni, koma anachita kusankhidwa mwapadera ndi Mulungu monga mmene zinalili ndi Melekizedeki. (Aheb. 5:10) N’chifukwa chake lemba la Salimo 110:4 limati: “Yehova walumbira (ndipo sadzasintha maganizo). Iye wati: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale, monga mwa unsembe wa Melekizedeki!” Kuwonjezera pa udindo umene Yehova anamusankha kuti akakhale wansembe kumwamba, Yesu alinso ndi udindo wina monga mfumu, womwe anaulandira chifukwa chobadwira mumzera wa Davide. Yesu anakhala woyenera kulandira ufumuwu mogwirizana ndi pangano limene Yehova anachita ndi Davide. (2 Sam. 7:11-16) Choncho Yesu ali ndi maudindo awiri, ndi mfumu komanso wansembe ngati mmene zinalili ndi Melekizedeki.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 523 ¶5

Pangano

Kodi pangano la Chilamulo linakhala “lotha ntchito” m’njira yotani?

Tinganene kuti pangano la Chilamulo linakhala “lotha ntchito” pamene Mulungu anadziwitsa anthu zokhudza pangano latsopano kudzera mwa mneneri Yeremiya. (Yer. 31:31-34; Aheb. 8:13) Kenako mu 33 C.E., pangano la Chilamulo linathetsedwa pamene Khristu anaphedwa pamtengo wozunzikirapo (Akol. 2:14), ndipo pangano latsopano linayamba kugwira ntchito.​—Aheb. 7:12; 9:15; Mac. 2:1-4.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

it-1 524 ¶3-5

Pangano Latsopano

Pangano Latsopano. Mu 600 B.C.E., kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova ananeneratu za pangano latsopano. Iye ananena kuti panganoli lidzakhala losiyana ndi Pangano la Chilamulo lomwe Aisiraeli anaphwanya. (Yer. 31:31-34) Pa Nisani 14 mu 33 C.E., usiku woti Yesu aphedwa mawa lake, iye anakhazikitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Pa nthawiyi Yesu analengeza za pangano latsopano lomwe linkayenera kudzayamba kugwira ntchito chifukwa cha nsembe yake. (Luka 22:20) Patatha masiku 50 iye ataukitsidwa komanso masiku 10 atakwera kumwamba kwa Atate wake, Yesu anapereka mzimu woyera, umene analandira kuchokera kwa Yehova, kwa ophunzira ake omwe anasonkhana m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu.​—Mac. 2:1-4, 17, 33; 2 Akor. 3:6, 8, 9; Aheb. 2:3, 4.

M’pangano latsopanoli muli Yehova komanso “Isiraeli wa Mulungu,” yemwe akuimira odzozedwa omwe ndi ogwirizana ndi Khristu. Odzozedwawa ndi amene amapanga mpingo wa Khristu kapena kuti thupi lake. (Aheb. 8:10; 12:22-24; Agal. 6:15, 16; 3:26-28; Aroma 2:28, 29) Pangano latsopano linayamba kugwira ntchito pamene Yesu Khristu anakhetsa magazi ake ndi kukapereka mtengo wansembe yake kwa Yehova atakwera kumwamba. (Mat. 26:28) Munthu akasankhidwa kuti adzapite Kumwamba (Aheb. 3:1), Mulungu amagwiritsa ntchito nsembe ya mwana wake kuti munthuyo akhale nawo m’panganoli. (Sal. 50:5; Aheb. 9:14, 15, 26) Yesu Khristu ndi mkhalapakati wa pangano latsopano (Aheb. 8:6; 9:15) ndiponso Mbewu Yoyamba ya Abulahamu. (Agal. 3:16) Yesu amagwiritsa ntchito udindo wake monga mkhalapakati wa pangano latsopano, pothandiza onse amene ali m’panganoli kuti akhale mbali ya mbewu yeniyeni ya Abulahamu (Aheb. 2:16; Agal. 3:29) powakhululukira machimo. Yehova amaona kuti anthu amenewa ndi olungama.​—Aroma 5:1, 2; 8:33; Aheb. 10:16, 17.

Odzozedwawa omwe ndi abale ake a Khristu, amakhala ansembe aang’ono omwe amagwira ntchito ndi Mkulu wa Ansembe ndipo amakhala “ansembe achifumu.” (1 Pet. 2:9; Chiv. 5:9, 10; 20:6) Iwo amagwira ntchito yawo monga ansembe, yomwe ndi “ntchito yotumikira anthu” (Afil. 2:17), ndipo amadziwikanso kuti “atumiki a pangano latsopano.” (2 Akor. 3:6) Anthu osankhidwawa amafunika kutsatira mapazi a Khristu mosamala kwambiri ndiponso mokhulupirika mpaka imfa yawo. Akatero, Yehova amawapatsa mwayi wokhala ufumu wa ansembe komanso ngati anzake a Khristu olandira nawo cholowa cha moyo wakumwamba ndipo amawapatsa mphotho ya moyo womwe sungafe komanso kuonongeka. (1 Pet. 2:21; Aroma 6:3, 4; 1 Akor. 15:53; 1 Pet. 1:4; 2 Pet. 1:4) Cholinga cha panganoli n’chofuna kusonkhanitsa anthu odziwika ndi dzina la Yehova kuti akhale mbali ya “mbewu” ya Abulahamu. (Mac. 15:14) Anthuwa amakhala “mkwatibwi” wa Khristu ndipo amapanga gulu lomwe Khristu anachita nalo pangano la Ufumu kuti adzalamulire naye limodzi. (Yoh. 3:29; 2 Akor. 11:2; Chiv. 21:9; Luka 22:29; Chiv. 1:4-6; 5:9, 10; 20:6) Pangano latsopanoli lidzakhala likugwirabe ntchito mpaka onse omwe akupanga gulu la “Isiraeli wa Mulungu” ataukitsidwa n’kupatsidwa moyo womwe sungafe kumwamba. Madalitso omwe adzakhalepo chifukwa cha panganoli sadzatha. N’chifukwa chake panganoli limadziwikanso kuti “pangano losatha.”​—Aheb. 13:20.

SEPTEMBER 9-15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 9-10

“Chithunzi cha Zinthu Zabwino Zimene Zikubwera”

it-1 862 ¶1

Kukhululuka

Malinga ndi lamulo limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, kuti munthu amene wachimwira Mulungu kapena mnzake akhululukidwe, choyamba ankafunika kukonza zimene walakwitsazo. Nthawi zambiri munthu wotere ankafunika kupereka nsembe ya nyama malinga ndi zimene Chilamulo chinkanena. (Lev. 5:5–6:7) N’chifukwa chake Paulo ananena kuti: “Inde, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi malinga ndi Chilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi anthu sangakhululukidwe machimo awo.” (Aheb. 9:22) Komabe, magazi a nyama sankayeretseratu machimowo n’kuchititsa kuti munthu akhale ndi chikumbumtima choyera. (Aheb. 10:1-4; 9:9, 13, 14) Mosiyana ndi zimenezi, pangano latsopano linachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu azikhululukidwa kotheratu pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu Khristu. (Yer. 31:33, 34; Mat. 26:28; 1 Akor. 11:25; Aef. 1:7) Ngakhale pamene anali padziko lapansi, Yesu anasonyeza kuti ali ndi udindo wokhululukira machimo pamene anachiritsa munthu wakufa ziwalo.​—Mat. 9:2-7.

it-2 602-603

Ungwiro

Chilamulo cha Mose Chinali Choperewera. Chilamulo chomwe Mulungu anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose chinkafuna kuti pakhale ansembe komanso kuti anthu azipereka nsembe zanyama zosiyanasiyana. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti ngakhale kuti Chilamulochi chinali chochokera kwa Mulungu ndipo chinali changwiro, Chilamulocho, ansembe komanso nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkathandiza anthu kukhala angwiro. (Aheb. 7:11, 19; 10:1) M’malo momasula anthu ku uchimo ndi imfa, Chilamulochi chinkachititsa kuti anthu adziwe kuti iwowo ndi ochimwa. (Aroma 3:20; 7:7-13) Ngakhale zili choncho, Chilamulo chinathandiza kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu chifukwa chinali ngati “mtsogoleri” wofikitsa anthu kwa Khristu ndipo chinkaimira “zinthu zabwino zimene zikubwera.” (Agal. 3:19-25; Aheb. 10:1) Choncho pamene Paulo ananena kuti Chilamulo ndi “chofooka chifukwa cha thupi” (Aroma 8:3), ankanena za kuperewera kwa mkulu wa ansembe wachiyuda (yemwe pogwiritsa ntchito Chilamulo ankapatsidwa udindo wotsogolera anthu pa nthawi yopereka nsembe komanso ndi amene ankalowa ndi magazi a nsembe m’Malo Oyera Koposa pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo) kuti ‘apulumutse kwathunthu’ anthu amene ankawaperekera nsembewo malinga ndi Aheberi 7:11, 18-28. Ngakhale kuti nsembe zimene zinkaperekedwa ndi ansembe a m’banja la Aroni zinkathandiza kuti anthu akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, nsembezi sizinkachotseratu uchimo. Mtumwi Paulo ananena kuti nsembe zimenezi sizinkapangitsa munthu “kukhala wangwiro m’chikumbumtima chake.” (Aheb. 10:1-4; yerekezerani ndi Aheb. 9:9.) Mkulu wa ansembe sankakwanitsa kupereka dipo limene likanawombola anthu ku uchimo mpaka kalekale. Ndi nsembe ya Khristu yokha imene inakwanitsa kuchita zimenezi.​—Aheb. 9:14; 10:12-22.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

w92 3/1 31 ¶4-6

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Paulo ananena kuti pankafunika kuperekedwa moyo kuti pangano la pakati pa Mulungu ndi anthu litheke. Chitsanzo cha zimenezi ndi pangano la Chilamulo. Mose ndi amene anali mkhalapakati wa panganoli pakati pa Mulungu ndi Aisiraeli. Mose anakwaniritsa udindo wofunika kwambiriwu pothandiza Aisiraeli kulowa m’panganoli. Koma kodi Mose ankafunika kupereka moyo wake kuti pangano la Chilamulo liyambe kugwira ntchito? Ayi. M’malo mwa magazi a Mose, magazi a nyama ndi amene ankaperekedwa.​—Aheberi 9:18-22.

Nanga bwanji za pangano latsopano la pakati pa Yehova ndi Isiraeli wauzimu? Yesu Khristu ndi amene ali mkhalapakati m’pangano la Yehova ndi Isiraeli wauzimu. Ngakhale kuti panganoli analiyambitsa ndi Yehova, Yesu anali ndi udindo waukulu wolikwaniritsa. Kuwonjezera pa kukhala mkhalapakati, Yesu ali padziko lapansi anagwira ntchito ndi anthu oyambirira kulowa m’panganoli. (Luka 22:20, 28, 29) Komanso iye ndi amene anali woyenerera kupereka nsembe yomwe inathandiza kuti panganoli liyambe kugwira ntchito. Iye sanapereke nsembe ya nyama koma anapereka moyo wake wangwiro. Choncho pangano latsopano linayamba kugwira ntchito Yesu atapereka moyo wake. Ichi n’chifukwa chake Paulo ananena za Khristu kukhala wochita pangano pamene anati: “Iye [Yesu] analowa . . . kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.”​—Aheberi 9:12-14, 24.

Pamene Paulo ankanena za Mose komanso Yesu kukhala ochita panganolo, sankatanthauza kuti Mose kapenanso Yesu ndi amene anayambitsa mapanganowo. Koma zoona zake n’zakuti anangokhala amkhalapakati a mapanganowa. Ndipo m’mapangano awiri onsewa magazi ankafunika. Mose sanapereke moyo wake, m’malomwake nyama ndi zimene zinkaperekedwa nsembe. Koma Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha anthu omwe anali m’pangano latsopano.

it-1 249-250

Ubatizo

Luka analemba kuti Yesu akubatizidwa, ankapemphera. (Luka 3:21) Choncho pamene Paulo ankauza Aheberi kuti Yesu Khristu “pobwera m’dziko” (sankatanthauza pa nthawi imene anabadwa popeza pa nthawiyi sakanatha kuwerenga kapena kulankhula mawu amenewa, koma panali pamene anabatizidwa n’kuyamba utumiki wake) ankanena zofanana ndi zimene lemba la Salimo 40:6-8 (LXX) lomwe limanena kuti: “Nsembe ndiponso zopereka, simunasangalale nazo ndipo munandipangira thupi . . . Ine ndabwera, pakuti mumpukutu munalembedwa za ine. Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.” (Aheb. 10:5-9) Yesu anabadwira mumtundu wachiyuda womwe unali kale m’pangano ndi Mulungu, lomwe ndi pangano la Chilamulo. (Eks. 19:5-8; Agal. 4:4) Pachifukwa chimenechi, tinganene kuti Yesu anali kale m’pangano ndi Yehova Mulungu pamene ankadzipereka n’kubatizidwa. Choncho pamenepa Yesu anachita zinthu zoposa zimene anayenera kuchita malinga ndi Chilamulo. Anadzipereka kwa Atate wake Yehova kuti achite “chifuniro” chake. Anachita zimenezi popereka thupi limene ‘anamukonzera’ ndipo zimenezi zinathetseratu nsembe zomwe zinkaperekedwa ndi ansembe. N’chifukwa chake mtumwi Paulo ananena kuti: “Mwa “chifuniro” chimenecho, tayeretsedwa kudzera m’thupi la Yesu Khristu loperekedwa nsembe kamodzi kokha.” (Aheb. 10:10) Mulungu ankafunanso kuti Yesu agwire ntchito yolengeza Ufumu mwakhama. Pa nkhani imeneyinso, Yesu anadzipereka ndi moyo wake wonse. (Luka 4:43; 17:20, 21) Yehova anakondwera ndi zimene Mwana wake anaperekazi ndipo anamudzoza ndi mzimu woyera n’kunena kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”​—Maliko 1:9-11; Luka 3:21-23; Mat. 3:13-17.

SEPTEMBER 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 11

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 804 ¶5

Chikhulupiriro

Zitsanzo Zakale za Anthu Achikhulupiriro. Anthu onse omwe ali mu “mtambo wa mboni waukulu” umene Paulo ankanena, (Aheb. 12:1) anali ndi zifukwa zomveka zokhalira ndi chikhulupiriro. Mwachitsanzo, Abele ayenera kuti ankadziwa za lonjezo la Mulungu lonena za “mbewu” yomwe inali kudzaphwanya mutu wa “njoka.” Komanso anaona umboni wa kukwaniritsidwa kwa chiweruzo chimene Mulungu anapereka kwa makolo ake mu Edeni. Atathamangitsidwa m’munda uja, Adamu ndi banja lake ankadya chakudya chochokera m’thukuta la nkhope yake chifukwa nthaka inali yotembereredwa moti inkangobereka minga ndi zitsamba zobaya. N’kuthekanso kuti Abele ankaona mayi ake akudandaula za bambo ake omwe ankangowapondereza. Sitikukaikiranso kuti ankamva mayi ake akudandaula za ululu umene ankamva pobereka. Komanso, Abele ankaona lupanga loyaka moto komanso akerubi omwe ankalondera munda wa Edeni. (Gen. 3:14-19, 24) Zonsezi zinali “umboni wooneka” womwe unathandiza Abele kukhulupirira kuti Mulungu adzapulumutsa anthu kudzera mwa ‘mbewu yolonjezedwa.’ Choncho, mwachikhulupiriro, Abele “anapereka kwa Mulungu nsembe” yamtengo wapatali kuposa ya Kaini.​—Aheb. 11:1, 4.

SEPTEMBER 23-29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 12-13

Kufufuza Mfundo Zothandiza

w89 12/15 22 ¶10

Muzipereka Nsembe Zimene Yehova Amakondwera Nazo

10 Aheberi ankayenera kuyesetsa kuti asatengeke ndi “ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo” za Ayuda Osunga Miyambo. (Agalatiya 5:1-6) Ziphunzitso zachilendozi zinali zosathandiza koma “kukoma mtima kwakukulu” kwa Mulungu ndi komwe kunkathandiza anthu kuti akhale ndi chikhulupiriro komanso kuti apitirize kutsatira mfundo za choonadi. Ena ankakangana pa nkhani ya zakudya komanso nsembe. Ichi n’chifukwa chake Paulo ananena kuti mtima sungakhale wolimba ndi “zakudya, pakuti amene amatanganidwa ndi zakudyazo sakupindula nazo.” Munthu amapeza madalitso ochokera kwa Yehova akakhala wodzipereka komanso ngati amayamikira nsembe ya Khristu. Koma sangapeze madalitso chifukwa cha zakudya komanso kusunga masiku ena ake. (Aroma 14:5-9) Ndiponso nsembe ya Khristu inapangitsa kuti nsembe zimene Alevi ankapereka zisiye kugwira ntchito.​—Aheberi 9:9-14; 10:5-10.

SEPTEMBER 30–​OCTOBER 6

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YAKOBO 1-2

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 253-254

Kuwala

Yehova ndi “Atate wa zounikira zonse zakuthambo.” (Yak. 1:17) Sikuti iye wangokhala “wopereka dzuwa kuti liziwala masana, woikira mwezi malamulo, wopereka nyenyezi kuti ziziwala usiku,” (Yer. 31:35) koma amatiphunzitsanso kuti timudziwe bwino. (2 Akor. 4:6) Malamulo a Mulungu, zigamulo zake komanso mawu ake amakhala ngati kuwala kwa anthu amene amalola kuti ziwatsogolere. (Sal. 43:3; 119:105; Miy. 6:23; Yes. 51:4) Wolemba masalimo anati: “Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, tikuona kuwala.” (Sal. 36:9; yerekezerani ndi Sal. 27:1; 43:3.) Mofanana ndi kuwala kwa dzuwa kumene kumawonjezereka kuyambira m’bandakucha “mpaka tsiku litakhazikika,” ndi mmenenso njira ya olungama imapitirizira kuwala ndi nzeru yochokera kwa Mulungu. (Miy. 4:18) Timayenda n’kuwala kwa Yehova tikamatsatira zimene amatiuza. (Yes. 2:3-5) Koma munthu akamachita zoipa amasonyeza kuti ali mu mdima wauzimu. Yesu ananena kuti: “Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzachita mdima. Choncho ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima, ndiye kuti mdimawo ndi wandiweyani!”​—Mat. 6:23; yerekezerani ndi Deut. 15:9; 28:54-57; Miy. 28:22; 2 Pet. 2:14.

it-2 222 ¶4

Chilamulo

“Lamulo Lachifumu.” Limatchedwa “lamulo lachifumu” chifukwa mfumu imakhala yofunika kwambiri kuposa anthu ake. Mofanana ndi zimenezi, lamulo loti tizikonda anzathu ndi lofunika kwambiri kuposa malamulo ena. (Yak. 2:8) Mfundo yaikulu ya Pangano la Chilamulo inali chikondi. Ndipo Chilamulocho chinkanena kuti “uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” Ndipo lamuloli (lamulo lachifumu) linali mbali yachiwiri ya lamulo lomwe panachokera malamulo onse opezeka m’Chilamulo ndi Zolemba za Aneneri. (Mat. 22:37-40) Ngakhale kuti Akhristu sali m’pangano la Chilamulo, amamvera lamulo la Yehova ndi Mwana wake Yesu Khristu, omwe ndi mafumu mogwirizana ndi mfundo za m’pangano latsopano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena