Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
OCTOBER 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YAKOBO 3-5
“Muzisonyeza Nzeru Yochokera kwa Mulungu”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Chikhulupiriro Chimatithandiza Kukhala Oleza Mtima Komanso Olimbikira Kupemphera
8 Kunenera Mkhristu mnzathu zinthu zoipa ndi tchimo. (Yakobo 4:11, 12) Komabe ena amakonda kupezera zifukwa Akhristu anzawo, mwina chifukwa choti amadziona kuti iwowo ndi olungama kwambiri. Enanso amanyoza anzawo kuti iwowo azioneka ngati anthu abwino kuposa anzawowo. (Salimo 50:20; Miyambo 3:29) Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti ‘kunenera,’ amanena za chidani ndipo amatanthauza kusinjirira nkhani kapena kunenera wina mabodza. Anthu amene amachita zimenezi amakhala akuweruza abale awo molakwika. Ndiye n’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu wotere amakhala “akunenera zoipa lamulo ndi kuweruza lamulo”? Alembi ndi Afarisi ‘ankanyalanyaza malamulo a Mulungu,’ n’kumaweruza anthu pogwiritsa ntchito malamulo awo. (Maliko 7:1-13) Mofanana ndi zimenezi, ngati tikuweruza Mkhristu mnzathu yemwe Yehova sanamuweruze, kodi sitinganene kuti ‘tikuweruza malamulo a Mulungu’ ndipo tikuona kuti malamulowo ndi operewera? Choncho tikamangokhalira kupezera zifukwa abale athu timakhala tikulephera kukwaniritsa lamulo la chikondi.—Aroma 13:8-10.
OCTOBER 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 PETULO 1-2
“Khalani Oyera”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 565 ¶3
Woyang’anira
Woyang’anira Wathu Wamkulu. Lemba la 1 Petulo 2:25 liyenera kuti linagwira mawu a pa Yesaya 53:6 pomwe pamanena za anthu omwe ‘akungoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa.’ Kenako Petulo ananena kuti: “Koma tsopano mwabwerera kwa m’busa wanu ndi woyang’anira miyoyo yanu.” Pamenepa Petulo ankanena za Yehova Mulungu. Tikutero chifukwa anthu amene Petulo ankawalembera kalatayi ankatsatirabe Yesu Khristu komanso anali atabwereranso kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi M’busa Wamkulu wa anthu ake, kudzera mwa Yesuyo. (Sal. 23:1; 80:1; Yer. 23:3; Ezek. 34:12) Kuwonjezera pamenepa, tinganenenso kuti Yehova ndi woyang’anira chifukwa amafufuza mitima yathu. (Sal. 17:3) Palembali mawu akuti kufufuza (m’Chigiriki, e·pi·sko·peʹ) akusonyeza kuti nthawi zina Yehova angachite zimenezi kuti aone zimene zalakwika n’kupereka chilango ngati mmene anachitira pamene ankawononga mzinda wa Yerusalemu, womwe ‘sunazindikire kuti nthawi yoyendera [m’Chigiriki, e·pi·sko·peʹ] inali itakwana.’ (Luka 19:44) Kufufuza kumeneku kungatanthauzenso kuyendera n’cholinga choona zabwino zimene zikuchitika n’kupereka madalitso ngati mmene zinakhalira kwa anthu omwe ankatamanda Mulungu “m’tsiku lake loyendera [m’Chigiriki, e·pi·sko·peʹ].”—1 Pet. 2:12.
OCTOBER 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 PETULO 3-5
“Mapeto a Zinthu Zonse Ayandikira”
Mmene Mungadziwire ndi Kuthetsera Chofooka Chilichonse Chauzimu
Pomaliza, nthawi zonse muzikumbukira malangizo achikondi a mtumwi Petulo akuti: “Koma mapeto a zinthu zonse ayandikira. Choncho khalani oganiza bwino, ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera. Koposa zonse, khalani okondana kwambiri, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Petulo 4:7, 8) N’zosavuta kuti zolakwa zathu kapena za anthu ena zitikhumudwitse n’kutilepheretsa kuchita zambiri potumikira Mulungu. Satana amadziwa bwino zimenezi. Choncho amagwiritsa ntchito msampha umenewu pofuna kusokoneza mgwirizano wathu kuti atigwire mosavuta. Ndiyetu m’pofunika kuti tizikwirira machimo a abale athu powakhululukira komanso kuwakonda ndi mtima wonse ndipo ‘tisamam’patse malo Mdyerekezi.’—Aefeso 4:25-27.