Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
NOVEMBER 4-10
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 YOHANE 1-5
“Musamakonde Dziko Kapena Zinthu za M’dziko”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 862 ¶5
Kukhululuka
N’zofunika kumapempherera anzathu komanso Akhristu ena onse kuti Mulungu aziwakhululukira machimo awo. Nthawi ina Mose anapemphereranso mtundu wa Isiraeli. Iye anavomereza zolakwa zomwe anthuwo anachita ndi kupempha Yehova kuti awakhululukire ndipo Yehova anayankha pemphero lake. (Num. 14:19, 20) Komanso pa nthawi imene Solomo ankapereka kachisi, anapempha Yehova kuti azikhululukira anthu ake akalapa n’kusiya njira zawo zoipa. (1 Maf. 8:30, 33-40, 46-52) Ezara nayenso anapereka pemphero loimira Ayuda onse lopempha Mulungu kuti awakhululukire pa zolakwa zimene anachita. Pemphero lake lochokera pansi pa mtima linalimbikitsa Ayuda kuti asinthe zochita zawo kuti Mulungu awakhululukire. (Ezara 9:13–10:4, 10-19, 44) Patapita nthawi, Yakobo analemba mawu olimbikitsa munthu amene akudwala mwauzimu kuti auze akulu a mumpingo kuti amupempherere, ndipo anati, “ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.” (Yak. 5:14-16) Komabe Baibulo limati palinso “tchimo lobweretsa imfa.” Limeneli ndi tchimo lochimwira mzimu woyera, kutanthauza kuchimwa mwadala ndipo munthu ameneyu sangakhululukidwe. Mkhristu sayenera kupempherera anthu ngati amenewa.—1 Yoh. 5:16; Mat. 12:31; Aheb. 10:26, 27.
NOVEMBER 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 YOHANE 1–YUDA
“Tiyenera Kuchita Khama Kuti Tikhalebe m’Choonadi”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 279
Maphwando Osonyezana Chikondi
Baibulo silifotokoza zambiri zokhudza maphwando amenewa komanso nthawi imene ankachitika. (Yuda 12) Yesu Khristu komanso atumwi ake sanalamule anthu kuti azichita maphwandowa ndipo n’zodziwikiratu kuti anthu sankakakamizidwa kuti aziwachita. Ena amanena kuti Akhristu omwe anali olemera ankakonza maphwandowa ndipo ankaitana Akhristu anzawo omwe anali osauka. Pa nthawiyi, ana ndi akazi amasiye, olemera ndi osauka, onse ankasangalala kudyera limodzi.
it-2 816
Mwala
Mawu enanso achigiriki akuti spi·las,ʹ amanena za mwala kapena thanthwe lomwe lili pansi pa madzi. Yuda anagwiritsa ntchito mawuwa ponena za anthu ena amene analowa mumpingo wachikhristu ndi zolinga zolakwika. Monga mmene miyala yapansi pa madzi inkachititsira ngozi sitima za pamadzi, anthu amenewanso ankasokoneza anthu ena mumpingo. Yuda anafotokoza kuti: “Anthu amenewa ali ngati miyala ikuluikulu yobisika m’madzi, pamene akudya nanu limodzi pa maphwando anu amene mumachita kuti musonyezane chikondi.”—Yuda 12.