Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 September tsamba 7
  • “Pitirizani Kuganizira Zimenezi”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Pitirizani Kuganizira Zimenezi”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhulupirika Kumagwirizana ndi Zimene Timaganiza
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • “Zimene Ndimaganizira Mozama”
    Imbirani Yehova Mosangalala
  • Kodi Tingawonjezere Motani Ukoma Pachikhulupiriro Chathu?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kusinkhasinkha
    Galamukani!—2014
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 September tsamba 7
M’bale ali pakompyuta yake usiku komanso mkango, womwe ukuimira Satana, ukubangula kumbuyo kwake

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Pitirizani Kuganizira Zimenezi”

Kuganizira chiyani? Lemba la Afilipi 4:8 limati, tiziganizira zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika. Komabe sikuti Akhristu amafunika kuti azingoganizira za Baibulo basi. Akhoza kumaganiziranso zinthu zina, koma ziyenera kukhala zimene Yehova angasangalale nazo. Sitiyenera kuganizira zinthu zomwe zingatichititse kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova.​—Sal. 19:14.

Nthawi zina zimakhala zovuta kuti tisamaganizire zinthu zoipa. Zili choncho chifukwa timalimbana ndi thupi lathu lochimwali komanso Satana yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4) Popeza Satana ndiye wolamulira wadzikoli, zinthu zambiri zomwe zimapezeka pa intaneti, m’mabuku komanso zimene zimaulutsidwa pawailesi kapena pa TV zimakhala zoipa. Ngati sitingasankhe bwino, zinthu zimenezi zikhoza kuwononga maganizo athu ndipo n’kupita kwa nthawi tingayambe kuchita zoipa.​—Yak. 1:14, 15.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAWONONGE KHALIDWE LANU LA KUKHULUPIRIKA​—ZOSANGALATSA ZOSAYENERA. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • M’bale akuonera zinthu zokayikitsa pafoni yake usiku

    Kodi m’bale wa m’vidiyoyi amaonera zinthu zotani pafoni yake, nanga zinamukhudza bwanji?

  • M’bale akuchotsa pulogalamu yochezera ndi anthu pa intaneti

    Kodi lemba la Agalatiya 6:7, 8 ndi Salimo 119:37, linamuthandiza bwanji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena