MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amakonda Anthu Aukhondo
Makolo ambiri amakonda kuuza ana awo kuti, ‘Kasambeni m’manja. Kakonzeni kuchipinda kwanu. Kaseseni panja. Katayeni zinyalala.’ Amanena zimenezi kuti anawo azikhala aukhondo. Yehova nayenso amafuna kuti tizikhala aukhondo. (Eks. 30:18-20; Deut. 23:14; 2 Akor. 7:1) Timasonyeza kuti timalemekeza Yehova tikamasamalira thupi komanso zinthu zathu. (1 Pet. 1:14-16) Koma nanga bwanji nkhani yosamalira pakhomo pathu komanso malo ena? Anthu ambiri amangotaya zinyalala paliponse koma Akhristufe timafunika kuonetsetsa kuti dzikoli, lomwe ndi malo athu okhala, ndi laukhondo. (Sal. 115:16; Chiv. 11:18) Zinthu zina zomwe zimaoneka ngati nkhani yaing’ono monga kutaya paliponse zitsipe zanzimbe, makoko achimanga kapena anthochi, mapepala amaswiti komanso mabotolo azakumwa, kungasonyeze kuti si ife anthu aukhondo. Choncho tiyenera kusonyeza m’mbali zonse za moyo wathu “kuti ndife atumiki a Mulungu.”—2 Akor. 6:3, 4.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MULUNGU AMAKONDA ANTHU AUKHONDO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi anthu ena amapereka zifukwa zotani akamalephera kusamalira zinthu zawo kuti zikhale zaukhondo?
Kodi Chilamulo cha Mose chinasonyeza bwanji kuti Yehova amafuna kuti anthu ake azikhala aukhondo?
Kodi tikamakhala aukhondo, timathandiza bwanji anthu ena kuti azilemekeza Yehova?
Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimaona ukhondo kukhala wofunika kwambiri ngati mmene Yehova amachitira?