CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 PETULO 3-5
“Mapeto a Zinthu Zonse Ayandikira”
Posachedwapa chisautso chachikulu chomwe sichinayambe chachitikapo, chiyamba. Kodi tingatani kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu panopa nthawiyi isanafike?
Tizipemphera nthawi zonse pogwiritsa ntchito mitundu yonse ya pemphero
Tizikonda abale ndi alongo athu ndipo tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana kwambiri
Tizikhala ochereza
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndi njira zina ziti zomwe ndingasonyezere kuti ndimakonda kwambiri abale, nanga ndingasonyeze bwanji mtima wochereza kwa abale ndi alongo a m’dziko lathu komanso ochokera m’mayiko ena?’