MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Dziko “Linameza Mtsinje”
Kuyambira kale, olamulira a dziko akhala akuthandiza anthu a Yehova. (Ezara 6:1-12; Esitere 8:10-13) Ngakhale masiku ano “dziko,” lomwe likuimira anthu a maganizo oyenera omwe ali ndi mphamvu m’dzikoli, limameza “mtsinje” wamavuto amene “njoka,” yomwe ndi Satana Mdyerekezi, amabweretsera atumiki a Yehova. (Chiv. 12:16) Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amatipulumutsa,” amatha kugwiritsa ntchito olamulira a dzikoli kuti athandize anthu ake.—Sal. 68:20; Miy. 21:1.
Nanga bwanji ngati munamangidwa chifukwa cha zimene mumakhulupirira? Musakayikire kuti Yehova akuona zimene zikukuchitikirani. (Gen. 39:21-23; Sal. 105:17-20) Musamakayikirenso kuti Yehova adzakudalitsani kwambiri komanso musamaiwale kuti kukhulupirika kwanu kumalimbikitsa abale ndi alongo padziko lonse.—Afil. 1:12-14; Chiv. 2:10.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ABALE A KU KOREA ATULUTSIDWA M’NDENDE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
N’chifukwa chiyani abale ambiri a ku South Korea ankamangidwa?
Kodi khoti linagamula zotani kuti abale athu atulutsidwe m’ndende?
Kodi tingathandize bwanji abale athu padziko lonse omwe ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo?
Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito bwanji ufulu umene tili nawo panopa?
Kodi ndi ndani amene amatithandiza kuti tipambane milandu yosiyanasiyana?
Kodi ndimagwiritsa ntchito bwanji ufulu umene ndili nawo panopa?