MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mungafotokoze Bwanji Zimene Mumakhulupirira?
Kodi munthu atakufunsani kuti n’chiyani chimakupangitsani kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa, mungamuyankhe bwanji? Kuti muyankhe bwino funsoli, mungafunike kuchita zinthu ziwiri izi: Choyamba, inuyo panokha muyenera kutsimikizira kaye kuti zinthu zinachita kulengedwa. (Aroma 12:1, 2) Ndipo chachiwiri, muyenera kudziwa mmene mungafotokozere zomwe mumakhulupirirazo.—Miy. 15:28.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, DOKOTALA WOONA ZA MAFUPA AKUFOTOKOZA ZA CHIKHULUPIRIRO CHAKE KOMANSO YAKUTI KATSWIRI WOONA ZA ZINTHU ZAMOYO AKUFOTOKOZA ZA CHIKHULUPIRIRO CHAKE, KUTI MUONE ZIFUKWA ZIMENE ZINACHITITSA ANTHU ENA KUYAMBA KUKHULUPIRIRA KUTI ZINTHU ZINACHITA KULENGEDWA. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
N’chifukwa chiyani Irène Hof Laurenceau anayamba kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa?
N’chifukwa chiyani Yaroslav Dovhanych anayamba kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa?
Munthu wina atakufunsani chifukwa chake mumakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa, kodi mungafotokoze bwanji?
Kodi gulu linatulutsa zinthu ziti m’chinenero chanu zomwe zingakuthandizeni inuyo komanso anthu ena kudziwa kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse?