CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 9-11
“Dziko Lonse Lapansi Linali ndi Chilankhulo Chimodzi”
Pansanja ya Babele, Yehova anabalalitsa anthu osamvera posokoneza chilankhulo chawo. Masiku ano iye akusonkhanitsa khamu lalikulu lochokera m’mitundu komanso zinenero zonse n’kuwapatsa “chilankhulo choyera” kuti “onse aziitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.” (Zef. 3:9; Chiv. 7:9) “Chilankhulo choyera” chimenechi ndi choonadi chopezeka m’Baibulo chokhudza Yehova komanso zolinga zake.
Kuphunzira chilankhulo kumafuna zambiri osati kungoloweza mawu atsopano. Munthu akamaphunzira chilankhulo amafunika kuyamba kuganiza m’njira yatsopano. Mofanana ndi zimenezi, tikamaphunzira chilankhulo choyera cha choonadi, kaganizidwe kathu kamayamba kusintha. (Aroma 12:2) M’kupita kwa nthawi tonse timayamba kuganiza mofanana ndipo zimenezi zimathandiza kuti tizigwirizana kwambiri.—1 Akor. 1:10.