CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 15-17
N’chifukwa Chiyani Yehova Anasintha Dzina la Abulamu ndi Sarai?
Yehova ankaona kuti Abulamu anali munthu wolungama. Pamene ankamufotokozera zokhudza lonjezo lake, Yehova anapatsa Abulamu ndi Sarai mayina omwe anali ndi tanthauzo lokhudza zomwe zidzachitike m’tsogolo.
Mogwirizana ndi mayina awo, Abulahamu anakhala tate wa mitundu yambiri ndipo Sara anakhala mayi wa mafumu.
Abulahamu
Tate wa Mitundu Yambiri
Sara
Mfumukazi
Pamene tinabadwa, sitinasankhe dzina loti tipatsidwe. Koma mofanana ndi Abulahamu ndi Sara tingapange tokha mbiri imene tikufuna kukhala nayo. Dzifunseni kuti:
‘Kodi ndingatani kuti Yehova azindiona kuti ndine wolungama?’
‘Kodi mbiri yanga ndi yotani pamaso pa Yehova?’