CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 36-37
Yosefe Anachitiridwa Nsanje
Zimene zinachitikira Yosefe zikusonyeza zinthu zoipa zomwe zimachitika chifukwa cha nsanje yosayenera. Gwirizanitsani malemba ndi zifukwa zomwe zili m’munsimu zotichititsa kuthetsa maganizo alionse a nsanje yosayenera omwe tingakhale nawo.
LEMBA
CHIFUKWA
Anthu a nsanje sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu
Nsanje imasokoneza mtendere ndi mgwirizano mumpingo
Nsanje imativulaza
Nsanje imatilepheretsa kuona zabwino mwa anthu ena
Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingatichititse kuti tiyambe kuchita nsanje?