CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 4-5
“Ine Ndidzakhala Nawe Polankhula”
Yehova anathandiza Mose kuti asiye kuchita mantha. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa zimene Yehova anauza Mose?
Tizipewa mtima wodzikayikira
Tizidalira Yehova kuti akhoza kutipatsa chilichonse chomwe tingafune kuti tikwanitse utumiki wathu
Kukhulupirira Mulungu kungatithandize kuti tisamaope anthu
Kodi Yehova wandithandiza bwanji kuthana ndi mavuto pogwira ntchito yolalikira?