MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzidzichepetsa Ena Akamakuyamikirani
Nthawi zina anthu ena akhoza kutiyamikira. Zimenezi zikhoza kutilimbikitsa ngati kuyamikirako kukuchokera pansi pamtima komanso ngati kuli ndi zolinga zabwino. (Miy 15:23; 31:10, 28) Koma tikuyenera kusamala kuti kuyamikiridwako kusatichititse kuyamba kunyada kapena kumadziona ngati ndife oposa anthu ena.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIKHALA OKHULUPIRIKA NGATI MMENE YESU ANALILI—PAMENE ANTHU ENA AKUKUYAMIKIRANI, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi anthu angatiyamikire pa zinthu ziti?
Kodi abale aja anamuyamikira bwanji Sergei?
Kodi kuyamikira kwawo kunapitirira bwanji malire?
Kodi mwaphunzira chiyani mukaganizira mmene Sergei anayankhira modzichepetsa?