MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amateteza Anthu Ake
Chikondwerero cha Pasika woyamba chinali chofunika kwambiri. Usiku umenewo, Farao ataona kuti mwana wake woyamba kubadwa wafa, anauza Mose kuti: “Nyamukani, chokani pakati pa anthu anga, inuyo ndi ana onse a Isiraeli. Pitani, katumikireni Yehova, monga momwe mwanenera.” (Eks 12:31) Pa nthawiyi Yehova anasonyeza kuti amateteza anthu ake.
Tikaganizira mbiri ya atumiki a Yehova a masiku ano, n’zoonekeratu kuti Yehova akupitiriza kutsogolera komanso kuteteza anthu ake. Zimenezi zinafotokozedwa bwino kumalo osungirako zinthu zakale otchedwa “Anthu Odziwika ndi Dzina la Yehova” omwe ali kulikulu la padziko.
ONERANI VIDIYO YAKUTI KUONA MALO OSUNGIRAKO ZINTHU ZAKALE KU WARWICK: “ANTHU ODZIWIKA NDI DZINA LA YEHOVA,” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kuyambira mu 1914, kodi Ophunzira Baibulo anayamba kugwiritsa ntchito njira yatsopano iti pofuna kuthandiza anthu kuti azikhulupirira Baibulo, nanga njirayi inathandiza bwanji?
Kodi Ophunzira Baibulo anakumana ndi mayesero otani mu 1916 ndi 1918, nanga panali umboni wotani wosonyeza kuti Yehova ankatsogolera gulu lake?
Kodi n’chiyani chinathandiza anthu a Yehova kukhalabe okhulupirika ngakhale kuti ankatsutsidwa?
Kodi ndi mfundo yatsopano iti imene anthu a Yehova anauzidwa mu 1935, nanga zimenezi zinawakhudza bwanji?
Ngati munakaona malo osungira zinthu zakale amenewa, kodi n’chiyani chinakutsimikizirani kuti Yehova akutsogolera komanso kuteteza anthu ake?