CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 19-20
Mmene Malamulo 10 Amakukhudzirani
Akhristu satsatira Chilamulo cha Mose. (Akl 2:13, 14) Ndiye kodi Malamulo 10 komanso Chilamulo chonse zili ndi phindu lililonse kwa ife masiku ano?
Amasonyeza mmene Yehova amaonera zinthu
Amasonyeza zimene Yehova amayembekezera kuti tizichita
Amasonyeza mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu anzathu
Kodi Malamulo 10 amakuphunzitsani chiyani za Yehova?