CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 29-30
Chopereka kwa Yehova
Pamene chihema chinkamangidwa, anthu onse, kaya olemera kapena osauka, anali ndi mwayi wopereka ndalama zothandizira pa kulambira Yehova. Kodi masiku ano tingapereke bwanji kwa Yehova? Njira imodzi ndi kupereka ndalama zothandizira pomanga kapena kukonza Nyumba za Ufumu, Malo a Misonkhano, maofesi a omasulira mabuku, nyumba za Beteli kapena nyumba zina zimene zimagwiritsidwa ntchito polambira Yehova.
Kodi malemba otsatirawa amatiphunzitsa chiyani pa nkhani yopereka ndalama zothandizira pa kulambira koona?