Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 October tsamba 5
  • Achinyamata, Kodi Yehova Ndi Mnzanu Wapamtima?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata, Kodi Yehova Ndi Mnzanu Wapamtima?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Akhoza Kukhala Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mulungu Akukuitanani Kuti Mukhale Bwenzi Lake
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Kodi Ndikaulule Tchimo la Mnzanga?
    Galamukani!—2008
  • Kodi Bwenzi Langa Lapamtima Linasamukiranji?
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 October tsamba 5
M’bale wachinyamata wakhala padesiki pake ndipo akuphunzira payekha.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Achinyamata, Kodi Yehova Ndi Mnzanu Wapamtima?

Kodi mumafuna kuti mnzanu akhale ndi makhalidwe otani? Mwina mumafuna kuti akhale wokhulupirika, wokoma mtima komanso wopatsa. Yehova ali ndi makhalidwe onsewa. (Eks 34:6; Mac 14:17) Iye amamvetsera mukamapemphera, amakuthandizani mukamavutika komanso amakukhululukirani mukalakwitsa. (Sl 18:19, 35; 1Yo 1:9) Apa zikuonekeratu kuti Yehova ndi Mnzanu wabwino kwambiri.

Koma kodi mungatani kuti mukhale mnzake wa Yehova? Muyenera kuphunzira za iye powerenga Mawu ake. Muyeneranso kumuuza zakukhosi kwanu. (Sl 62:8; 142:2) Muzisonyeza kuti mumakonda zinthu zimene iye amaona kuti n’zofunika monga Mwana wake, Ufumu wake komanso malonjezo ake okhudza m’tsogolo. Muziuzanso anthu ena za iye. (De 32:3) Mukamayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, iye adzakhala Mnzanu mpaka kalekale.​—Sl 73:25, 26, 28.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ACHINYAMATA​—“TALAWANI NDIPO MUONA KUTI YEHOVA NDI WABWINO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi chamuvidiyo yakuti ‘Achinyamata​—Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova ndi Wabwino.’ Mlongo wachitsikana akupemphera asanayambe kuphunzira payekha.

    Kodi mungakonzekere bwanji kuti mudzadzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa?

  • Chithunzi chamuvidiyo yakuti ‘Achinyamata​—Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova ndi Wabwino.’ M’bale yemwe ndi mpainiya akuwerengera lemba munthu m’chinenero cha Chikareni (S’gaw).

    Kodi anthu ena mumpingo angakuthandizeni bwanji kuti muzitumikira Yehova?

  • Chithunzi chamuvidiyo yakuti ‘Achinyamata​—Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova ndi Wabwino.’ M’bale amene amayamikira thandizo la achikulire walowa ndi m’bale wachikulire mu utumiki.

    Kodi kulalikira kumalimbitsa bwanji ubwenzi wanu ndi Yehova?

  • Chithunzi chamuvidiyo yakuti ‘Achinyamata​—Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova ndi Wabwino.’ Pambuyo poyenda maola awiri wapansi kuchokera kwawo, mlongo akuphunzira ndi mtsikana amene ali ndi vuto losamva.

    Ubwenzi wanu ndi Yehova ungakhalepo mpaka kalekale

    Kodi pali zinthu ziti zimene mungachite potumikira Yehova?

  • Kodi mumakonda zinthu ziti zokhudza Yehova?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena