CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 16-17
Kodi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo Limakukhudzani Bwanji?
Kodi tikuphunzira chiyani pa mmene ansembe ankagwiritsira ntchito zofukiza pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo?
Mapemphero ovomerezeka a atumiki okhulupirika a Yehova ali ngati zofukiza. (Sl 141:2) Mkulu wa ansembe ankapereka zofukiza kwa Yehova mwaulemu kwambiri. Ifenso tikamapemphera kwa Yehova tiyenera kusonyeza kuti timamulemekeza kwambiri
Mkulu wa ansembe ankafunika kuika zofukiza pamoto asanapereke nsembe. Mofanana ndi zimenezi, Yesu asanapereke nsembe yake anafunika kusonyeza kuti anali wokhulupirika. Izi zinathandiza kuti Yehova alandire nsembe yakeyo
Kodi ndingatani kuti nsembe zanga zikhale zovomerezeka kwa Yehova?