Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsamba 5
  • Tetezani Banja Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tetezani Banja Lanu
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Ngati Ukwati Ukufuna Kusweka
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 January tsamba 5
Bambo wakhala pansi ndi mkazi wake ndipo onse akuchapa zovala mosangalala.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tetezani Banja Lanu

Yehova amaona kuti malumbiro a ukwati ndi nkhani yaikulu. Iye ananena kuti mwamuna ndi mkazi wake sayenera kusiyana. (Mt 19:​5, 6) M’gulu la Yehova muli mabanja ambiri osangalala. Komabe, palibe banja limene silikumana ndi mavuto. Tisamakhale ndi maganizo amene anthu ambiri ali nawo oti ngati m’banja muli mavuto, njira yabwino ndi kupatukana kapena kulithetsa. Ndiye kodi Akhristu angateteze bwanji banja lawo?

Mfundo 5 zotsatirazi zingathandize kwambiri.

  1. Muziteteza mtima wanu popewa zinthu monga kukopana komanso zosangalatsa zosayenera chifukwa zimenezi zingawononge banja lanu.​—Mt 5:28; 2Pe 2:14.

  2. Muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu ndipo muziyesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa m’banja lanu.​—Sl 97:10.

  3. Pitirizani kuvala umunthu watsopano ndipo muzimuchitira mnzanuyo zinthu zing’onozing’ono zosonyeza kukoma mtima. Zimenezi zingachititse kuti azisangalala.​—Akl 3:​8-10, 12-14.

  4. Muzilankhulana mwaulemu komanso mochokera pansi pa mtima.​—Akl 4:6.

  5. Muzipereka mangawa a m’banja kwa mnzanuyo mwachikondi.​—1Ak 7:​3, 4; 10:24.

Akhristu akamalemekeza banja, amakhala kuti akulemekezanso Yehova, yemwe analiyambitsa.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, TIYENERA ‘KUTHAMANGA MOPIRIRA’​—MUZITSATIRA MALAMULO A MPIKISANO NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Tiyenera ‘Kuthamanga Mopirira’​—Muzitsatira Malamulo a Mpikisano.’ M’bale ndi Mlongo Calou akumwetulira pambuyo pa nkhani ya ukwati wawo m’Nyumba ya Ufumu.

    Ndi mavuto ati amene banja lingakumane nawo ngakhale kuti linayamba bwinobwino?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Tiyenera ‘Kuthamanga Mopirira’​—Muzitsatira Malamulo a Mpikisano.’ M’bale ndi Mlongo Calou akukambirana mavuto awo modekha. Baibulo lotsegula lili patebulo.

    Kodi mfundo za m’Baibulo zingathandize bwanji anthu amene akuona kuti m’banja mwawo mulibe chikondi?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Tiyenera ‘Kuthamanga Mopirira’​—Muzitsatira Malamulo a Mpikisano.’ M’bale Calou akuwerengera mkazi wake komanso ana awo awiri buku lakuti, ‘Buku Langa la Nkhani za Baibulo.’

    Muzitsatira mfundo za m’Baibulo kuti mukhale ndi banja losangalala

    Kodi Yehova anakhazikitsa malamulo ati okhudza banja?

  • Kuti banja liziyenda bwino, kodi mwamuna komanso mkazi ayenera kumachita chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena