Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 9/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Banja?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Tetezani Banja Lanu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Mmene Mungakhalire ndi Banja Losangalala
    Galamukani!—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 9/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi mabanja angatani kuti azikhala osangalala?

Malangizo a m’Baibulo okhudza banja amathandiza kuti banja likhale losangalala chifukwa malangizowo amachokera kwa Yehova Mulungu, yemwe anayambitsa ukwati. Baibulo limatiphunzitsa kuti tizikhala ndi makhalidwe abwino amene angapangitse kuti banja likhale losangalala. Komanso limatichenjeza kuti tizipewa makhalidwe oipa amene angasokoneze banja lathu. Baibulo limatiphunzitsanso zimene tingachite kuti tizilankhulana bwino m’banja zomwe zimathandizanso kuti banja likhale losangalala.—Werengani Akolose 3:8-10, 12-14.

Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kulemekezana. Aliyense akamakwaniritsa udindo umene Mulungu anam’patsa, banja lawo limakhala losangalala.—Werengani Akolose 3:18, 19.

N’chiyani chingathandize kuti banja likhale lolimba?

Banja likhoza kukhala lolimba ngati mkazi ndi mwamuna amakondana. Mulungu komanso Yesu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Iwo amadzipereka kwambiri posonyeza chikondi.—Werengani 1 Yohane 4:7, 8, 19.

Banja likhoza kukhala lolimba ngati mwamuna ndi mkazi amaona kuti Mulungu ndi amene anayambitsa banja. Mulungu safuna kuti banja lizitha n’cholinga choti anthu a m’banjamo azikhala otetezeka. Mulungu anapanga amuna ndi akazi m’njira yoti azigwirizana pochita zinthu. Anawapanganso m’chifaniziro chake kuti azimutsanzira posonyezana chikondi.—Werengani Genesis 1:27; 2:18, 24.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 14 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lomwe ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Mukhozanso kupanga dawunilodi www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena