Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fg phunziro 9 mafunso 1-5
  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?
  • Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Banja?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
fg phunziro 9 mafunso 1-5

PHUNZIRO 9

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?

1. Kodi kukwatirana motsatira malamulo kumathandiza bwanji kuti banja likhale losangalala?

Mwamuna ndi mkazi akulembetsa ukwati wawo kuboma

Yehova, Mulungu wachimwemwe, amafuna kuti mabanja azikhala osangalala, ndipo umenewu ndi uthenga wabwino. (1 Timoteyo 1:11) Iye ndi amene anayambitsa ukwati. Kukwatirana motsatira malamulo kumathandiza kuti banja likhale losangalala chifukwa chakuti limakhala malo abwino olereramo ana. Choncho Akhristu ayenera kulemekeza malamulo a boma okhudza kulembetsa ukwati.​—Werengani Luka 2:1, 4, 5.

Kodi Mulungu amaona bwanji ukwati? Mulungu amafuna kuti mwamuna ndi mkazi okwatirana azikhala limodzi moyo wawo wonse. Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi amene ali pabanja, onse azikhala okhulupirika m’banjamo. (Aheberi 13:4) Iye amadana ndi kuthetsa ukwati. (Malaki 2:16) Komabe amalola kuti Mkhristu athetse ukwati wake n’kukwatirana ndi munthu wina ngati mnzake m’banjamo wachita chigololo.​—Werengani Mateyu 19:3-6, 9.

2. Kodi mwamuna ndi mkazi wake ayenera kumakhala motani?

Banja losangalala

Yehova analenga mwamuna ndi mkazi kuti azithandizana m’banja. (Genesis 2:18) Mwamuna, yemwe ndi mutu wa banja, ali ndi udindo waukulu wopezera banja lake zinthu zofunika komanso kuliphunzitsa zokhudza Mulungu. Mwamuna ayenera kusonyeza chikondi chololera kuvutikira mkazi wake. Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukondana kwambiri komanso kulemekezana. Popeza kuti onse, mwamuna ndi mkazi, ndi anthu opanda ungwiro, ayenera kuphunzira kukhululukirana ndipo zimenezi zidzawathandiza kuti azikhala osangalala m’banja.​—Werengani Aefeso 4:31, 32; 5:22-25, 33; 1 Petulo 3:7.

3. Ngati banja silikuyenda bwino, kodi ndi bwino kungolithawa?

Ngati mukuona kuti m’banja mwanu muli mavuto, aliyense wa inu ayesetse kusonyeza mnzake chikondi. (1 Akorinto 13:4, 5) Mawu a Mulungu salimbikitsa anthu okwatirana kuti azipatukana n’cholinga chothana ndi mavuto a m’banja mwawo.​—Werengani 1 Akorinto 7:10-13.

4. Ananu, kodi Mulungu amafuna kuti muzichita chiyani?

Makolo akuchita zinthu ndi ana awo panyumba

Yehova amafuna kuti ananu muzikhala osangalala. Iye wakupatsani malangizo abwino kwambiri okuthandizani kuti muzisangalala pamene muli achinyamata. Mulungu akufuna kuti mupindule ndi nzeru za makolo anu komanso zinthu zimene iwowo akumana nazo pa moyo. (Akolose 3:20) Yehova, yemwe ndi Mlengi wanu, akufunanso kuti muzisangalala pochita zinthu zimene iye komanso Mwana wake akufuna.​—Werengani Mlaliki 11:9–12:1; Mateyu 19:13-15; 21:15, 16.

5. Inu makolo, kodi mungatani kuti ana anu azikhala osangalala?

Bambo akulankhula ndi mwana wake

Muyenera kuyesetsa kuwapezera chakudya, pokhala ndiponso zovala. (1 Timoteyo 5:8) Koma kuti ana anuwo azikhala osangalala, muyeneranso kuwaphunzitsa kukonda Mulungu ndiponso kutengera chitsanzo chake. (Aefeso 6:4) Ngati inuyo mumakonda Mulungu, chitsanzo chanu chidzathandiza kwambiri ana anu kuti nawonso azikonda kwambiri Mulungu. Mukamalangiza ana anu pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, mungawathandize kwambiri anawo kuti aziona zinthu moyenera.​—Werengani Deuteronomo 6:4-7; Miyambo 22:6.

Zimakhala zothandiza kwambiri kwa ana mukamawalimbikitsa komanso kuwayamikira. Koma akalakwitsa amafunika kuwapatsa chilango kapena kuwadzudzula. Zimenezi zingathandize kuti anawo azipewa makhalidwe omwe angachititse kuti azikhala osasangalala. (Miyambo 22:15) Komabe, si bwino kupatsa mwana chilango chokhwima kwambiri kapena kumulanga mwankhanza.​—Werengani Akolose 3:21.

A Mboni za Yehova ali ndi mabuku osiyanasiyana omwe cholinga chake n’kuthandiza makolo komanso ana. Mfundo za m’mabuku amenewa ndi zochokera m’Baibulo.​—Werengani Salimo 19:7, 11.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 14 m’buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena