Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsamba 7
  • Misonkhano Yachigawo Imatipatsa Mwayi Wosonyezana Chikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yachigawo Imatipatsa Mwayi Wosonyezana Chikondi
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amasonkhanitsa Anthu Ake Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mboni za Yehova Zidzakhala ndi Misonkhano ya Mitundu Yonse
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Misonkhano ya Mayiko mu 2003
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Tinali Osiyana Zinenero Koma Chikondi Chinatigwirizanitsa”
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 January tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Misonkhano Yachigawo Imatipatsa Mwayi Wosonyezana Chikondi

Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana akujambulitsa pamsonkhano wa mayiko.

N’chifukwa chiyani timasangalala kwambiri ndi misonkhano yachigawo? Mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Aisiraeli, pamisonkhanoyi timakhala ndi mwayi wolambira Yehova limodzi ndi Akhristu anzathu ambirimbiri. Timaphunzira mfundo zambiri zimene zimatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Timakhalanso ndi mwayi wocheza ndi achibale komanso anzathu. Chifukwa choti timaona kuti misonkhanoyi ndi yofunika kwambiri, timayesetsa kupezekapo masiku onse atatu.

Tikakhala ndi msonkhano, tisamangoganizira mmene ungatithandizire ifeyo. Koma tiziganiziranso mmene tingasonyezere chikondi kwa anzathu. (Aga 6:10; Ahe 10:​24, 25) Timasonyeza kuti sitimangoganizira zofuna zathu zokha, tikamachita zinthu monga kutsegulira ena chitseko kapena kupewa kusunga malo omwe sitiwagwiritsa ntchito. (Afi 2:​3, 4) Pamisonkhano yachigawo timakhala ndi mwayi wopeza anzathu atsopano. Tingachite bwino kukhala ndi cholinga choti msonkhano usanayambe, pa nthawi yopuma kapena ukatha, tidziwane ndi munthu wina. (2Ak 6:13) Anthu amene tingadziwane nawo pa nthawiyi, akhoza kukhala anzathu mpaka kalekale. Chinanso n’chakuti anthu akaona kuti timakondana kwambiri, nawonso angayambe kutumikira Yehova.​​​—Yoh 13:35.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, MSONKHANO WAMAYIKO WAKUTI “CHIKONDI SICHITHA” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Msonkhano Wamayiko Wakuti ‘Chikondi Sichitha.’’ Abale ndi alongo ochokera m’mayiko osiyanasiyana akukumbatirana ndiponso kulandirana ndi abale a m’dzikolo pamsonkhano wa mayiko.

    Kodi abale ndi alongo amene anapita kumisonkhano ya mayiko ya 2019 anasonyezedwa bwanji chikondi?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Msonkhano Wamayiko Wakuti ‘Chikondi Sichitha.’’ Abale ndi alongo a m’dzikolo akujambulitsa ndi abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena.

    N’chifukwa chiyani mgwirizano komanso chikondi chimene anthu a Mulungu amasonyezana zili zapadera?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Msonkhano Wamayiko Wakuti ‘Chikondi Sichitha’’ Abale ndi alongo a ku Korea akulandira anthu obwera ku msonkhano.

    Kodi abale a m’Bungwe Lolamulira anasonyeza bwanji chikondi?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Msonkhano Wamayiko Wakuti ‘Chikondi Sichitha’’ Mtsikana wanyamula ‘Baibulo la Dziko Latsopano’ lomwe walandira pamsonkhano ndipo akusangalala.

    Kodi inuyo mungachite zinthu ziti pothandiza kuti chikondi chimene timasonyezana pamisonkhano yachigawo chipitirire?

    Kodi chikondi chinathandiza bwanji abale a ku Germany ndi ku South Korea kuti akhale ogwirizana?

  • Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena