Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 4/1 tsamba 29
  • Mboni za Yehova Zidzakhala ndi Misonkhano ya Mitundu Yonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova Zidzakhala ndi Misonkhano ya Mitundu Yonse
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Misonkhano ya Mayiko mu 2003
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Yehova Amasonkhanitsa Anthu Ake Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Misonkhano Yachigawo Imatipatsa Mwayi Wosonyezana Chikondi
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 4/1 tsamba 29

Mboni za Yehova Zidzakhala ndi Misonkhano ya Mitundu Yonse

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likulinganiza kudzakhala ndi misonkhano ya mitundu yonse mu 1998. Chilengezo chimenechi chinawasangalatsa omwe anali pamsonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, womwe unachitikira mu Nyumba Yamsonkhano ku Jersey City pa Loŵeruka, October 5, 1996.

Limodzi ndi misonkhano yachigawo ya nthaŵi zonse, misonkhano ya mitundu yonse idzachitikira ku North America chapakati pa 1998. Tikuyembekezera kuti misonkhano imeneyi idzasonkhanitsa Mboni zikwi zochuluka zochokera kumadera ambiri padziko lapansi. Kuti atheketse maiko ambiri kukhala ndi owaimira, nthambi iliyonse ya maofesi a Watch Tower Society oposa 100 idzatumiza gulu la nthumwi ku msonkhano wa mitundu yonse ku mzinda womwe adzasankha ku North America.

Mwachionekere, si onse amene angapite ku North America ngakhale atafuna kupita. Komabe, nkotheka kuti anthu zikwi zambiri apezeke pamsonkhano wa mitundu yonse wapafupi ndi kwawo. Tikupanga makonzedwe oti misonkhano ya mitundu yonse ichitikire m’maiko aŵiri kapena atatu ku Ulaya ndi ina idzachitikira mu Afirika, Asia, Latin America, South Pacific, ndi ku Caribbean.

Panthaŵi yoyenera, maofesi a nthambi za Sosaite azadziŵitsa mipingo ya m’magawo ake za mzinda kapena mizinda ya msonkhanowo kumene awaitanira. Chidziŵitso chidzaperekedwa ponena za madeti a msonkhano ndi makonzedwe a kasankhidwe ka nthumwizo. Amene akuganiza zofunsira kusankhidwa monga nthumwi angayambe kumasunga ndalama zawo zina poyembekezera zochitika zapadera zimenezi.

Mboni za Yehova zonse padziko lonse lapansi zingayembekezere kuona zomwe zikutidikira pamisonkhano ya mitundu yonse imeneyi ya 1998. Misonkhano yachigawo m’maiko onse idzakhala ndi programu yofanana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena