Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 March tsamba 5
  • Kodi Mukukonzekera Chikumbutso?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukonzekera Chikumbutso?
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndiitane Ndani?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira Ine”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • “Muzichita Zimenezi” Chikumbutso Chidzachitika pa April 5
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 March tsamba 5
Petulo ndi Yohane akuika mkate ndi makapu patebulo.

Chithunzi chapachikuto: Petulo ndi Yohane akukonza chipinda cham’mwamba choti muchitikire Pasika wa mu 33 C.E.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mukukonzekera Chikumbutso?

Mwambo wa Pasika womaliza umene Yesu anachita unali wofunika kwambiri. Chifukwa choti anali atatsala pang’ono kuphedwa, anakonza zoti adye Pasika ndi atumwi ake kenako n’kuyambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye woti uzichitika chaka chilichonse. Choncho anatuma Petulo ndi Yohane kuti akakonze chipinda choti achitiremo mwambowu. (Lu 22:7-13; onani chithunzi cha pachikuto.) Zimenezi zikutikumbutsa kufunika kokonzekera Chikumbutso chomwe chidzachitike pa 27 March. Mipingo iyenera kuti yakonzekera kale zokhudza wokamba nkhani, zizindikiro komanso zinthu zina. Komabe kodi ndi zinthu ziti zimene aliyense payekha angachite pokonzekera?

Muzikonzekeretsa mtima wanu. Muziwerenga ndiponso kuganizira malemba a pa nyengo ya Chikumbutso. Ndandanda ya malemba amenewa mungaipeze mu kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku. Ndandanda ina yokhala ndi zambiri mungaipeze mu Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu. (Onaninso Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu ya April 2020) Mabanja angapeze mfundo zokambirana pa kulambira kwa pabanja zokhudza kufunika kwa dipo pofufuza mu Watch Tower Publications Index kapena mu Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani.

Banja likukambirana zokhudza Chikumbutso pa kulambira kwa pabanja.

Muziitanira ena. Muzigwira nawo mwakhama ntchito yoitanira anthu ku mwambowu. Ganizirani za anthu amene mungawaitane monga maulendo obwereza, amene munkaphunzira nawo Baibulo, amene mumadziwana nawo komanso achibale. Akulu ayenera kuonetsetsa kuti aitanira anthu amene anasiya kusonkhana. Musaiwale kuti ngati munthu sakhala m’dera lanu, mungathe kupeza nthawi ndi malo amene Chikumbutso chichitikire kwawoko podina pamene alemba kuti ZOKHUDZA IFEYO pa jw.org pamwamba pa tsamba loyamba. Kenako sankhani pomwe alemba kuti “Chikumbutso.”

Akulu awiri ayendera m’bale amene anafooka ndipo akumuitanira ku Chikumbutso.

Ndi zinthu zinanso ziti zomwe tingachite pokonzekera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena