CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzithawira ‘M’manja a Yehova Amene Adzakhalapo Mpaka Kalekale’
Yehova amafuna kuti nthawi zonse tizisonyeza makhalidwe abwino (De 33:26; it-2 51)
Yehova amatithandiza ndi mtima wonse pogwiritsa ntchito mphamvu zake (De 33:27; w11 10/15 26 ¶18)
Mofanana ndi Mose, tiyenera kukhulupirira kuti Yehova amapulumutsa anthu ake (De 33:29; w11 9/15 19 ¶16)
Manja a Yehova amene adzakhalapo mpaka kalekale amatithandiza tikamakumana ndi mayesero osiyanasiyana. Zimenezi zikuphatikizapo tikadwala kapena tikamavutika maganizo, tikaferedwa kapena tikalakwitsa zinazake n’kulapa.