Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 September tsamba 3-16
  • Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Ndi Buku Lakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” mu Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Ndi Buku Lakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” mu Utumiki
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mungaphunzitsire ndi Buku la “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale”
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 September tsamba 3-16
Banja likugwiritsa ntchito kabuku kakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” ndipo likukambirana ndi bambo wina pamalo okwerera basi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Ndi Buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale mu Utumiki

Ndife osangalala kwambiri kuti tili ndi kabuku komanso buku latsopano lomwe tizigwiritsa ntchito pochititsa maphunziro a Baibulo. Tikupempha Yehova kuti atidalitse pamene tikuyesetsa kuphunzitsa anthu ambiri. (Mt 28:18-20; 1Ak 3:6-9) Kodi tizigwiritsa ntchito bwanji zinthu zatsopanozi?

Buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale lizitithandiza kuphunzira Baibulo ndi anthu mochita kukambirana. M‘bukuli muli njira yatsopano yophunzitsira anthu, choncho mukamakonzekera komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo muzigwiritsa ntchito njira zotsatirazi.a

  • Muziwerenga ndime komanso kukambirana mafunso

  • Muziwerenga malemba akuti “werengani” ndipo muzimuthandiza wophunzirayo kumvetsa mmene angawagwiritsire ntchito

  • Muzionera komanso kukambirana mavidiyo pogwiritsa ntchito mafunso amene aperekedwa

  • Muziyesetsa kumaliza phunziro lililonse pa ulendo umodzi

Tikakhala mu utumiki tiziyamba ndi kugawira kabuku kuti tione ngati munthu ali ndi chidwi. (Onani bokosi lakuti “Zimene Tingachite Kuti Tigawire Kabuku Kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pa Ulendo Woyamba.”) Ngati mwamaliza kuphunzira limodzi kabukuka ndipo wophunzirayo akufuna kupitiriza kuphunzira, muzimugawira buku ndi kuyamba kuphunzira naye phunziro 04. Ngati mukuphunzira ndi munthu pogwiritsa ntchito buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa kapena lakuti Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani, yambani kuphunzira naye buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale n’kuona pamene mungayambire.

Banja lomwe lija likugwiritsa ntchito buku lakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” pochititsa phunziro la Baibulo ndi bambo yemwe uja kunyumba kwake.

ONERANI VIDIYO YAKUTI SANGALALANI POPHUNZIRA BAIBULO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi anthu aziphunzira chiyani m’buku latsopanoli?

  • N’chifukwa chiyani muyenera kumuonetsa vidiyoyi wophunzira watsopano?

  • Kodi ndi zolinga ziti zimene muyenera kumulimbikitsa wophunzira kukhala nazo komanso kuzikwaniritsa?​—Onani tchati chakuti “Cholinga cha Chigawo Chilichonse Komanso Zomwe Wophunzira Akulimbikitsidwa Kuchita.”

a DZIWANI IZI: Ngakhale kuti mukhoza kusankha kugwiritsa ntchito kachigawo kakuti “Onani Zinanso” pa nthawi ya phunziro, muziyesetsa kupeza nthawi yowerenga komanso kuonera mavidiyo onse pamene mukukonzekera. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwa zimene zingafike pamtima komanso kuthandiza wophunzira wanuyo. M’kabuku komanso m’buku la pazipangizo zamakono muli malinki a mavidiyo komanso zinthu zina zowonjezera.

CHOLINGA CHA CHIGAWO CHILICHONSE KOMANSO ZOMWE WOPHUNZIRA AKULIMBIKITSIDWA KUCHITA

—

PHUNZIRO

CHOLINGA CHAKE

ZOMWE WOPHUNZIRA AKULIMBIKITSIDWA KUCHITA

1

01-12

Kukambirana mmene Baibulo lingakuthandizireni komanso zimene mungachite kuti mudziwe amene analilemba

Kuwerenga Baibulo, kukonzekera phunziro komanso kuyamba kupezeka pamisonkhano

2

13-33

Kukambirana zimene Mulungu watichitira komanso kulambira kumene kumamusangalatsa

Kuuza ena mfundo za choonadi komanso kukhala wofalitsa

3

34-47

Kukambirana zimene Mulungu amafuna kuti anthu omwe amamulambira azichita

Kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa

4

48-60

Kuphunzira zimene mungachite kuti Mulungu apitirize kukukondani

Kuphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIGAWIRE KABUKU KAKUTI MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE PA ULENDO WOYAMBA

Mofanana ndi timapepala tathu, kumapeto kwa kabukuka kulinso funso lochititsa chidwi. Tayeserani kuchita zotsatirazi:

  • Funsani funso

  • Werengani yankho la m’Baibulo lomwe likupezeka pa Salimo 37:29

  • Kambiranani mfundo zomwe zikupezeka pansi pa funso lakuti “Kodi Zimenezi Zikutanthauza Chiyani?” Ngati nthawi ilipo, werengani malemba komanso kambiranani zithunzi

  • M’pempheni kuti mukambirane funso lomaliza patsambali, ndipo yambani kuphunzira naye phunziro loyamba m’kabukuka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena