MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zinthu Zothandiza Zomwe Zili M’buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale
Kodi mumakonda kugwiritsa ntchito mavidiyo komanso mafunso a m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale omwe amathandiza munthu kufotokoza maganizo ake? Nanga bwanji mbali zina ngati “Zimene Ena Amanena,” “Zolinga” komanso “Onani Zinanso”? Ndi zinthu zinanso ziti zimene mumaona kuti zimakuthandizani mukamagwira ntchito yophunzitsa anthu?—Mt 28:19, 20.
Mavidiyo ndi Zinthu Zina: Ngati mumakonda kugwiritsa ntchito buku losindikizidwa pochititsa phunziro la Baibulo, kodi mungatani kuti mupeze mavidiyo ndi zinthu zina zonse pamalo amodzi? M’buku la pazipangizo zamakono sankhani chigawo chimodzi pa zigawo 4 zomwe zili m’bukuli. Pansi penipeni pa mitu ya maphunziro, mukhoza kupeza mavidiyo komanso zinthu zina zimene zili m’chigawocho. (Onani chithunzi 1)
Batani la “Printed Edition”: Ngati mukuphunzira ndi munthu pogwiritsa ntchito buku la pachipangizo chamakono, mwina nthawi zina pa nthawi ya phunzirolo mungakonde kuona la “Printed Edition.” Mukatsegula phunzirolo dinani timadontho titatu tomwe tili pamwamba mbali ya kumanja kenako dinani pamene alemba kuti “Printed Edition.” Zikatero tsamba lonse limaoneka pa sikirini ndipo zimakuthandizani kuti mugwirizanitse mfundo zonse za mu phunzirolo mosavuta. Kuti mubwerere ku buku la pachipangizo chamakono dinaninso timadontho titatu tija ndipo pitani pa “Digital Edition.”
“Kodi Ndakonzeka?”: Mabokosi awiri amenewa omwe ali chakumapeto kwa bukuli, ali ndi mfundo zomwe zingathandize wophunzira kudziwa ngati ali woyenerera kuyamba kulalikira limodzi ndi mpingo komanso kubatizidwa. (Onani chithunzi 2.)
Mawu Akumapeto: Mawu akumapeto amafotokozera mfundo zikuluzikulu zomwe zili m’bukuli. M’buku la pachipangizo chamakono, kumapeto kwa mawu akumapeto alionse, kumakhala linki yomwe imakutengeraninso ku phunziro limene munapezako mawu akumapetowo. (Onani chithunzi 2.)
Muzionetsetsa kuti mwamaliza kuphunzira buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale ngakhale wophunzirayo atabatizidwa. Muziperekerabe lipoti phunzirolo, nthawi komanso maulendo obwereza ngakhale pambuyo poti wophunzirayo wabatizidwa. Ngati mwapita ku phunziroko ndi wofalitsa wina ndipo nayenso anaphunzitsa nawo, aziwerengera nthawi