Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsamba 11
  • Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvera Chisoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvera Chisoni
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?
    Galamukani!—2010
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Yehova “Amachiritsa Anthu Osweka Mtima”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 September tsamba 11

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvera Chisoni

Nthawi zina, tonsefe timakhumudwa. Koma kukhumudwa sikutanthauza kuti tayamba kufooka mwauzimu. Ndipotu ngakhale Yehova, nthawi zina amakhumudwa. (Ge 6:​5, 6) Koma bwanji ngati timakhala okhumudwa kwambiri nthawi zina kapenanso nthawi zonse?

Muzipemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni. Yehova amachita chidwi ndi zimene tikuganiza komanso mmene tikumvera mumtima. Amadziwa ngati tikusangalala kapena ngati takhumudwa. Amamvetsa zimene zimatichititsa kuti tiziganiza kapena kumva mmene tikumvera. (Sl 7:9b) Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti, Yehova amatidera nkhawa ndipo angatithandize pamene takhumudwa kapena pamene tikudwala matenda ovutika maganizo.—Sl 34:18.

Muziteteza maganizo anu. Kukhala ndi maganizo olakwika kungachititse kuti tisamasangalale komanso kungasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho tiyenera kumateteza mtima wathu kapena kuti umunthu wathu wamkati kuphatikizapo mmene timaganizira komanso mmene timamvera.—Miy 4:23.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MMENE ABALE ATHU AKUKHALIRA MWAMTENDERE NGAKHALE KUTI AKUVUTIKA MAGANIZO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Nikki anachita chiyani kuti apirire pamene ankavutika maganizo?

  • N’chifukwa chiyani Nikki anaona kuti akufunika thandizo lachipatala?—Mt 9:12

  • Kodi Nikki anasonyeza kuti amadalira Yehova m’njira ziti?

“Nsanja ya Olonda” Na. 1 2023, yamutu wakuti “Matenda Amaganizo​—⁠Mmene Baibulo Lingakuthandizireni.”

Kodi mukudziwa aliyense amene Nsanja ya Olonda yogawira Na. 1 2023 ingamuthandize?

Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite zomwe zingatithandize kuti tizikhala osangalala?

(Chongani zinthu zimene mukufunika kuti muzichita bwino.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena