Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsamba 13
  • Muzithandiza Anthu Osapembedza Kudziwa Mlengi Wawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Anthu Osapembedza Kudziwa Mlengi Wawo
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Amene Sakonda Zachipembedzo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Tizigwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Fufuzani Umboni
    Galamukani!—2021
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 September tsamba 13
Mlongo akulalikira mzimayi wa ku Asia.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzithandiza Anthu Osapembedza Kudziwa Mlengi Wawo

Kodi mumalephera kulalikira anthu osapembedza poganiza kuti mwina samvetsera uthenga wanu? Ngati ndi choncho, muzikumbukira kuti anthu ambiri amene sanali m’chipembedzo chilichonse, kuphatikizapo amene ankati kulibe Mulungu, anakhala a Mboni za Yehova. Nthawi zambiri anthu amenewa amangofunika kuwathandiza kupeza umboni woti kuli Mulungu.—Aro 1:20; 10:14.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ANTHU OPANDA CHIKHULUPIRIRO AKHOZA KUSINTHA N’KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO—ANTHU OSAPEMBEDZA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

Kodi zomwe zinachitikira Tommaso zakuthandizani bwanji kukhala ndi maganizo oyenera kuti muzilalikira kwa anthu osapembedza?

Mmene mungachitire zimenezi

Ngati munthu akusonyeza kuti sakukhulupirira kuti kuli Mulungu, muzikhala oleza mtima, ndipo mwanzeru komanso mochokera pansi pamtima, muzimusonyeza kuti mukumvetsa mmene akumvera pa nkhani imene mukukambirana. (2Ti 2:24) Muzikambirana naye nkhani zimene mukuona kuti akhoza kuchita nazo chidwi. Kodi angavomere kuti mukambirane naye maumboni amene athandiza anthu ena kuyamba kukhulupirira kuti kuli Mlengi? Ngati ndi choncho, gwiritsani ntchito mabuku kapena mavidiyo amene anakonzedwa kuti azithandiza anthu pa nkhani imeneyi. Timabuku takuti Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? ndi Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri, tinaikidwanso pa Zinthu Zophunzitsira kuti tizipezeka mosavuta.

Poyamba, mwina mungachite mantha kukambirana ndi munthu amene sakhulupirira Mulungu. Ngati ndi choncho, mukhoza kupempha wofalitsa waluso kuti akuthandizeni. Muzikumbukiranso kuti Yehova akhoza kukuthandizani kuti muzifika pamtima anthu a mtima wabwino, ngakhale atakhala kuti poyamba sankakhulupirira kuti iye alikodi. —Mac 13:48.

Kabuku kakuti “Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?”
Kabuku kakuti “Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri.”
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena