Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w21 February tsamba 25
  • Zonsezi N’chifukwa Cha Kumwetulira Basi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zonsezi N’chifukwa Cha Kumwetulira Basi
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kukumbukira Mlengi Wathu Kuyambira Paunyamata
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Amayi Amachita Ntchito Zambiri
    Galamukani!—2002
  • Kulalikira ndi Mashelefu Kwathandiza Anthu Ambiri Padziko Lonse
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi​​—Muziteteza Mgwirizano Wathu Wamtengo Wapatali
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
w21 February tsamba 25

Zonsezi N’chifukwa Cha Kumwetulira Basi

Helen akumwetulira ataima pafupi ndi kashelefu. Atsikana awiri akudutsa.

TSIKU lina atsikana awiri amayenda kumalo a zamalonda mumzinda wa Baguio ku Philippines. Iwo anaona a Mboni akulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu koma sanafike pamalopo. Mlongo amene anali pashelefupo dzina lake Helen, anawamwetulira. Atsikanawo anapitiriza ulendo wawo koma sanaiwale zimene Helen anachita powamwetulira.

Kenako atsikanawo ali m’basi pobwerera kwawo, anaona chikwangwani chachikulu cha jw.org pa Nyumba ya Ufumu. Iwo anakumbukira kuti zilembo zimenezi ndi zomwe anazionanso pakashelefu kaja. Ndiye anatsika basi n’kupita pageti la Nyumba ya Ufumuyo kukaona nthawi imene misonkhano imachitikira pa nyumbayo.

Atsikana awiri aja akumwetulira ataona Helen ku Nyumba ya Ufumu.

Atsikanawo anadzachita nawo msonkhano wotsatira pa Nyumba ya Ufumuyo. Iwo atalowa m’Nyumba ya Ufumuyo anadabwa kwambiri kuona Helen. Nthawi yomweyo anamuzindikira kuti ndi munthu amene anawamwetulira uja. Helen anati: “Pamene atsikanawo ankabwera pamene ndinali ndinayamba kuchita timantha. Ndinkaganiza kuti mwina pali zinazake zimene ndalakwitsa.” Koma atsikanawo anafotokozera Helen kuti anamuona ataima pakashelefu.

Atsikanawo anasangalala kuchita nawo msonkhanowo komanso kucheza ndi abale ndi alongo. Ataona anthu ena akukonza m’Nyumba ya Ufumuyo pambuyo pamsonkhanowo, anafunsa ngati angagwire nawo ntchitoyo. Mmodzi wa atsikanawo anachoka m’dzikolo koma winayo anayamba kusonkhana ndipo akuphunzira Baibulo. Zonsezi n’chifukwa cha kumwetulira basi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena