MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kulalikira ndi Mashelefu Kwathandiza Anthu Ambiri Padziko Lonse
Malinga ndi Machitidwe chaputala 5, Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankapita kukachisi komwe kunkapezeka anthu ambiri n’cholinga choti akalalikire uthenga wabwino. (Mac. 5:19-21, 42) Masiku ano njira yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri pogwiritsira ntchito kashelefu yathandiza anthu ambiri.
ONERANI VIDIYO YAKUTI KULALIKIRA NDI MASHELEFU KWATHANDIZA ANTHU AMBIRI PADZIKO LONSE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi njira yolalikira pogwiritsa ntchito kashelefu inayamba liti, nanga inayamba bwanji?
Kodi kulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kuli ndi ubwino wotani tikayerekezera ndi kugwiritsa ntchito tebulo?
Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Mi Jung You?
Kodi zimene zinachitikira Jacob Salomé zikusonyeza bwanji ubwino wolalikira pogwiritsa ntchito kashelefu?
Kodi zimene zinachitikira Annies ndi mwamuna wake zikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya mmene tingachitire tikamalalikira pogwiritsa ntchito kashelefu?