Tingalalikire Bwanji Pogwiritsa Ntchito Tebulo Kapena Kashelefu Kamatayala?
Kulalikira pogwiritsa ntchito tebulo kapena kashelefu kamatayala kukuthandiza kuti anthu ambiri a mitima yabwino aphunzire choonadi. (Yoh. 6:44) Choncho akulu anauzidwa kuti ayenera kukonza zoti mpingo wawo uzilalikira pogwiritsa ntchito njirayi pamalo opezeka anthu ambiri m’gawo la mpingo wawo. Popeza polalikira pogwiritsa ntchito njirayi sitimafunika kumanga kabenchi, nthawi zambiri sitingafunike kupempha chilolezo kwa akuluakulu a pamalopo. Ndiye kodi ndani ayenera kulalikira pogwiritsa ntchito njira imeneyi? Akulu ayenera kusankha ofalitsa amene amachita zinthu mozindikira, achitsanzo chabwino komanso amene ali ndi luso lolankhula ndi anthu. Mfundo zotsatirazi zikufotokoza zimene muyenera kuchita komanso zimene simuyenera kuchita mukamalalikira pogwiritsa ntchito njirayi.