Ndandanda ya Mlungu wa April 27
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 27
Nyimbo Na. 68 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 12 ndime 1-8 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 26-31 (Mph. 8)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aef. 5:15, 16.
Mph. 7: Tizikambirana ndi Munthu Mfundo za M’Malemba Mogwira Mtima. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 251 mpaka 253 ndime 1.
Mph. 10: Nyumba ya Ufumu Yosamalidwa Bwino Imachititsa Kuti Yehova Alemekezeke. Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Yehova ndi Mulungu woyera, choncho atumiki ake ayeneranso kuona kuti ukhondo ndi wofunika. (Eks. 30:17-21; 40:30-32) Tikamasamalira bwino Nyumba ya Ufumu zimapangitsa kuti Yehova alemekezeke. (1 Pet. 2:12) Tchulani zitsanzo zomwe zinachitika kudera lanulo kapena zomwe zili m’mabuku athu zosonyeza kuti tikamasamalira bwino Nyumba ya Ufumu, zimathandiza kuti anthu ena aphunzire za Yehova. Funsani m’bale yemwe amayang’anira ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu kuti afotokoze zimene mpingo wanu umachita posamalira nyumba yanu ya Ufumu. Limbikitsani onse kuti azithandiza nawo kusamalira Nyumba ya Ufumu.
Mph. 13: “Muzilengeza za Mphamvu ya Mawu a Mulungu mu Utumiki.” Nkhani yokambirana yomwe ili patsamba 4. Mukamaliza kukambirana nkhaniyi, chitani chitsanzo cha mbali ziwiri. Mbali yoyamba, wofalitsa akusonyeza munthu kabuku ka Uthenga Wabwino ndipo akutchula mawu ena ndi ena a palemba la 2 Timoteyo 3:16, 17 koma sakuwerenga kuchokera m’Baibulo. Kenako wofalitsayo akuchitanso chitsanzochi, koma ulendo uno akuwerenga lembalo kuchokera m’Baibulo. Pemphani omvera kuti afotokoze chifukwa chake kuchita zimene wofalitsa wachita m’chitsanzo chachiwirichi n’kothandiza.
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero