Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira April 27, 2015. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
Kodi munthu amene ali ndi chikondi chosatha amachita zotani ndipo timafunika kusonyeza chikondichi kwa ndani? (Rute 1:16, 17) [Mar. 2, w12 7/1 tsa. 26 ndime 6]
N’chiyani chinachititsa kuti Rute akhale “mkazi wabwino kwambiri?” (Rute 3:11) [Mar. 2, w12 10/1 tsa. 23 ndime 1]
Tikakhala pa mavuto, kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha Hana? (1 Sam. 1:16-18) [Mar. 9, w07 3/15 tsa. 16 ndime 4-5]
Samueli ali mwana ‘ankakula akukondedwa ndi Yehova.’ Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asatengere khalidwe loipa la ana a Eli? (1 Sam. 2:21) [Mar. 9, w10 10/1 tsa. 16 ndime 2-3]
Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Sauli anachita, posawachita chilichonse “anthu opanda pake” omwe ankamunyoza atakhala mfumu? (1 Sam. 10:22, 27) [Mar. 23, w05 3/15 tsa. 23 ndime 1]
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Sauli anachita, poganiza kuti nsembe inali yofunika kwambiri kuposa kumvera Yehova? (1 Sam. 15:22, 23) [Mar. 30, w07 6/15 tsa. 26 ndime 3-4]
N’chifukwa chiyani tingati n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova “amaona mmene mtima ulili”? (1 Sam. 16:7) [Apr. 6, w10 3/1 tsa. 23 ndime 7]
Mogwirizana ndi lemba la Miyambo 1:4, ndi makhalidwe ati amene Yehova amayembekezera kuti tiziwagwiritsa ntchito tikakumana ndi mavuto? (1 Sam. 21:12, 13) [Apr. 13, w05 3/15 tsa. 24 ndime 4]
Kodi zimene Abigayeli anachita, popatsa Davide ndi anyamata ake zinthu zomwe anapempha, zikusonyeza kuti sankagonjera mwamuna wake? Fotokozani. (1 Sam. 25:10, 11, 18, 19) [Apr. 20, w09 7/1 tsa. 20 ndime 3]
Abigayeli anapepesa kwa Davide ngakhale kuti iyeyo sanali wolakwa. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chakechi? (1 Sam. 25:24) [Apr. 20, w02 11/1 tsa. 5 ndime 1 4]