November 26–December 2
MACHITIDWE 6-8
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mpingo Watsopano Wachikhristu Unayesedwa”: (10 min.)
Mac. 6:1—Azimayi olankhula Chigiriki omwe anali amasiye ankasalidwa mumpingo (bt 41 ¶17)
Mac. 6:2-7—Atumwi anapeza njira yothetsera vutoli (bt 42 ¶18)
Mac. 7:58–8:1—Mpingo unayamba kuzunzidwa kwambiri
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mac. 6:15—Kodi nkhope ya Sitefano “inali ngati nkhope ya mngelo” m’njira yotani? (bt 45 ¶2)
Mac. 8:26-30—Kodi masiku ano Akhristu ali ndi mwayi wogwira ntchito yotani yofanana ndi imene Filipo anagwira? (bt 58 ¶16)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 6:1-15
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. Kenako muitanireni kumisonkhano yathu.
Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba lililonse ndipo gawirani buku kapena kabuku kamene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) lv 33 ¶16-17
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzipereka Mphatso kwa Yehova”: (15 min.) Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu. Yambani ndi kuonera vidiyo yakuti ‘Muzipereka Mphatso kwa Yehova’ Werengani kalata yochokera ku ofesi ya nthambi yosonyeza kuyamikira ndalama zimene abale ndi alongo anapereka chaka cha utumiki chapitachi. Fotokozani mmene timapindulira tikamapereka ndalama zathu. Tchulani ndalama zimene mpingo wanu umagwiritsa ntchito mwezi uliwonse. Kambiranani mmene tingaperekere ndalama zathu komanso mmene ndalama zimenezi zimagwirira ntchito. Yamikirani abale ndi alongo chifukwa cha mtima wawo wokonda kupereka.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 15
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 74 ndi Pemphero