CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 6-8
Mpingo Watsopano Wachikhristu Unayesedwa
Akazi amasiye olankhula Chigiriki omwe anali atangobatizidwa kumene, amene anakhalabe kwa kanthawi ku Yerusalemu, ankasalidwa. Kodi iwo anakhumudwa ndi zimenezi, kapena anadikira moleza mtima kuti Yehova athetse nkhaniyo?
Sitefano ataponyedwa miyala, komanso anthu atayamba kuzunza Akhristu a mumpingo wa ku Yerusalemu, ambiri anathawira ku Yudeya ndi ku Samariya. Koma kodi zimenezi zinachititsa kuti abwerere m’mbuyo pankhani yolalikira?
Ngakhale kuti mpingo wachikhristu unakumana ndi mavuto amenewa, unapitirizabe kukula chifukwa chakuti Yehova ankauthandiza.—Mac. 6:7; 8:4.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ineyo ndimatani ndikakumana ndi mayesero?’