Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 15 tsamba 40-tsamba 41 ndime 6
  • Chozizwitsa Choyamba Chimene Yesu Anachita

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chozizwitsa Choyamba Chimene Yesu Anachita
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Chozizwitsa Choyamba cha Yesu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Chozizwitsa Chachiwiri Chimene Yesu Anachita ku Kana
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Chozizwitsa Chachiŵiri Ali m’Kana
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 15 tsamba 40-tsamba 41 ndime 6
Ku ukwati wa ku Kana, Yesu akuuza anthu amene akutumikira kuti adzaze mbiya ndi madzi

MUTU 15

Chozizwitsa Choyamba Chimene Yesu Anachita

YOHANE 2:1-12

  • UKWATI UMENE UNACHITIKA KU KANA

  • YESU ANASANDUTSA MADZI KUKHALA VINYO

Yesu pamodzi ndi ena mwa ophunzira ake analowera chakumpoto ku Galileya patangodutsa masiku atatu kuchokera pamene Natanayeli anakhala mmodzi wa ophunzira ake oyambirira. Iwo ankapita ku tauni ya Kana komwe kunali kwawo kwa Natanayeli. Tauni ya Kana inali m’dera la mapiri kumpoto kwa mzinda wa Nazareti, kumene Yesu anakulira. Iwo ankapita kumeneko chifukwa anali ataitanidwa ku phwando la ukwati.

Mariya, yemwe anali amayi ake a Yesu, anapitanso ku ukwatiwo. Zikuoneka kuti Mariya ankadziwana ndi amene ankakwatiranawo ndipo ayenera kuti ankathandiza nawo ntchito yolandira komanso kusamalira alendo. N’chifukwa chake anazindikira mwamsanga kuti zinthu zina zinali zitatha ndipo anauza Yesu kuti: “Vinyo waathera.”—Yohane 2:3.

Ponena mawu amenewa, Mariya ankafuna kuti Yesu athandizepo. Poyankha, Yesu anagwiritsa ntchito mawu okuluwika osonyeza kuti akukana. Iye anati: “Kodi ndili nanu chiyani mayi?” (Yohane 2:4) Monga Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, cholinga cha Yesu chinali kuchita zimene Atate wake wakumwamba wamuuza, osati zimene abale ake kapena anzake amuuza. Mariya anangosiya nkhaniyi m’manja mwa mwana wake ndipo anauza anthu amene ankatumikira pa ukwatiwo kuti: “Chilichonse chimene angakuuzeni, chitani chimenecho.”—Yohane 2:5.

Pamalopo panali mbiya zamiyala zokwana 6 ndipo mbiya iliyonse inkatha kusunga madzi okwana malita 40. Yesu anauza anthu amene ankagwira ntchito pa ukwatipo kuti: “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Kenako anawauza kuti: “Tunganimo tsopano mupereke kwa woyang’anira phwandoli.”—Yohane 2:7, 8.

Woyang’anira phwando la ukwati akuyamikira mkwati chifukwa cha vinyo wabwino

Woyang’anira phwandoyo anasangalala kwambiri atalawa vinyoyo chifukwa anali wokoma kwambiri koma sanadziwe kuti vinyoyo anali atapangidwa mozizwitsa. Choncho anaitana mkwati n’kumuuza kuti: “Munthu aliyense amatulutsa vinyo wabwino choyamba, ndipo anthu akaledzera, m’pamene amatulutsa wosakoma kwenikweni. Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.”—Yohane 2:10.

Chimenechi chinali chozizwitsa choyamba chimene Yesu anachita. Ophunzira akewo ataona zimene Yesu anachitazi, anayamba kumukhulupirira kwambiri. Kenako Yesu, mayi ake ndi abale ake ananyamuka n’kupita ku Kaperenao, mzinda womwe unali m’mbali mwa nyanja ya Galileya, kumpoto chakumadzulo.

  • Kodi ukwati wa ku Kana unachitika liti?

  • Kodi Yesu ananena chiyani mayi ake atamuuza kuti vinyo watha?

  • Kodi Yesu anachita chozizwitsa chotani, ndipo zimenezi zinawakhudza bwanji ophunzira ake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena