Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w21 April tsamba 26-29
  • “Panopa Ndimakonda Kwambiri Utumiki”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Panopa Ndimakonda Kwambiri Utumiki”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NDINASIYA KUSANGALALA
  • NDINAPHUNZIRA MFUNDO YOFUNIKA KWAMBIRI
  • NDINAYAMBIRANSO KUKONDA KULALIKIRA
  • NDINAPEZA MNZANGA WOCHITA NAYE UPAINIYA
  • YEHOVA ANATIDALITSANSO KWAMBIRI
  • SINDIKANAPEZA MOYO WABWINO KUPOSA UMENEWU
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupemphera?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Yehova, Ndiloleni Kuti Ndikutumikireni”
    Galamukani!—2007
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kuyandikira kwa Mulungu Kunandithandiza Kulaka
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
w21 April tsamba 26-29
Vanessa Vicini.

MBIRI YA MOYO WANGA

“Panopa Ndimakonda Kwambiri Utumiki”

YOFOTOKOZEDWA NDI VANESSA VICINI

NDINAKULIRA m’tawuni ina yotchedwa Balclutha, ku South Island ku New Zealand. Ndili mwana ndinali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo ndinkakonda kwambiri choonadi. Ndinkakonda kupita kumisonkhano ndipo ndikakhala pakati pa abale ndi alongo ndinkaona kuti ndine wotetezeka komanso ndinkasangalala. Ngakhale kuti ndinali wamanyazi, ndinkakonda kupita kolalikira mlungu uliwonse. Sindinkachita mantha kulalikira kwa anzanga a kusukulu komanso anthu ena. Ndinkasangalala kuti ndine wa Mboni za Yehova ndipo nditakwanitsa zaka 11 ndinadzipereka kwa Mulungu.

NDINASIYA KUSANGALALA

N’zomvetsa chisoni kuti ndili ndi zaka pafupifupi 13, chikondi changa pa Yehova chinayamba kuchepa. Ndinayamba kuona kuti anzanga a kusukulu ali ndi ufulu wambiri ndipo nanenso ndinkafuna ufulu umenewo. Ndinkaona kuti malamulo a makolo anga komanso mfundo za Chikhristu n’zopanikiza, ndipo kulambira Yehova kunayamba kukhala chimtolo kwa ine. Ngakhale kuti sindinkakayikira kuti Yehova alipo, ndinkaona kuti sindili naye pa ubwenzi.

Sindinasiyiretu kulalikira, koma ndinkalalikira mwa apo ndi apo. Sindinkakonzekera ndikamapita kolalikira, choncho zinkandivuta kuti ndiyambe kapena kupitiriza kukambirana ndi munthu. Zimenezi zinachititsa kuti ndizingolalikira mwamwambo chabe komanso ndisamasangalale. Ndiye ndinkadzifunsa kuti, ‘Munthu angakwanitse bwanji kumachita zimenezi mlungu ndi mlungu komanso mwezi ndi mwezi?’

Nditakwanitsa zaka 17, ndinkafunitsitsa kukhala pandekha. Choncho ndinalongedza zikwama zanga, n’kuchoka pakhomo ndipo ndinapita ku Australia. Makolo anga anakhumudwa kwambiri kundiona ndikuchoka. Iwo ankadera nkhawa, komabe ankaganiza kuti ndikapitiriza kutumikira Yehova.

Ndili ku Australia, chikondi changa pa Yehova chinachepa kwambiri. Ndinayamba kujomba kumisonkhano. Ndinkagwirizana ndi achinyamata ena omwe ankati akapita kumisonkhano lero, mawa lake ankapita kumalo a zisangalalo kukamwa mowa komanso kuvina. Ndikaganizira za nthawi imeneyo, ndimaona kuti mwendo umodzi unali m’choonadi ndipo mwendo wina unali m’dzikoli, koma palibe mbali imene inkandisangalatsa.

NDINAPHUNZIRA MFUNDO YOFUNIKA KWAMBIRI

Patapita zaka pafupifupi ziwiri ndinakumana ndi mlongo wina yemwe sanadziwe kuti anandithandiza kuti ndiyambe kuganizira za moyo wanga. Tinkakhala nyumba imodzi alongo 5 omwe sitinali pabanja, ndipo tinaitana woyang’anira dera wina ndi mkazi wake Tamara, kuti adzakhale kunyumba kwathu kwa mlungu umodzi. Pamene mwamuna wake ankagwira ntchito zina zampingo, Tamara ankacheza nafe nkhani zosiyanasiyana komanso kuseka nafe. Zimenezi zinkandisangalatsa kwambiri. Iye anali wodzichepetsa komanso wochezeka. Ndinadabwa kuona kuti munthu amene ankakonda kwambiri kutumikira Yehova angamasangalale chonchi.

Tamara ankakonda kwambiri utumiki komanso choonadi. Ndipo zimenezi zinkalimbikitsanso ena kuti azichita zomwezo. Ndinkaona kuti iye ankasangalala kutumikira Yehova ndi mtima wake wonse, pomwe ine sindinkasangalala chifukwa sindinkachita zambiri pomutumikira. Khalidwe lake komanso chimwemwe chimene anali nacho zinakhudza kwambiri moyo wanga. Chitsanzo chake chabwino chinandithandiza kuganizira mfundo yofunika ya m’Malemba yakuti: Yehova amafuna kuti tonsefe tizimutumikira “mokondwera” komanso “tikufuula mosangalala.”​—Sal. 100:2.

NDINAYAMBIRANSO KUKONDA KULALIKIRA

Ndinkafuna kuti ndizisangalala ngati Tamara, koma kuti zimenezi zitheke ndinkafunika kusintha zinthu zambiri pa moyo wanga. Zinanditengera nthawi, koma pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kusintha. Ndinayambiranso kukonzekera ndikafuna kupita kolalikira ndipo kawirikawiri ndinkachita upainiya wothandiza. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisamachite mantha kwambiri komanso ndisamadzikayikire. Chifukwa chakuti ndinkagwiritsa ntchito kwambiri Baibulo ndikamalalikira, ndinkasangalala kwambiri ndi utumiki. Pasanapite nthawi ndinayamba kumachita upainiya wothandiza mwezi uliwonse.

Kenako ndinapeza anzanga a misinkhu yosiyanasiyana omwe ankakonda choonadi komanso ankasangalala kutumikira Yehova. Chitsanzo chawo chabwino chinandithandiza kuti ndiganizirenso zinthu zimene ndinkaona kuti n’zofunika kwambiri komanso kuti ndiyambe kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Ndinayamba kukonda kwambiri utumiki ndipo pasanapite nthawi ndinakhala mpainiya wokhazikika. Kwa nthawi yoyamba pambuyo pa zaka zambiri ndinayambiranso kukhala womasuka komanso wosangalala ndikakhala mumpingo.

NDINAPEZA MNZANGA WOCHITA NAYE UPAINIYA

Patatha chaka chimodzi ndinakumana ndi Alex, yemwe ndi munthu wokoma mtima, wokonda Yehova komanso wokonda utumiki. Pa nthawiyo anali mtumiki wothandiza ndipo anali atachita upainiya kwa zaka 6. Alex anatumikiraponso kudera lina lomwe kunkafunika olalikira ambiri ku Malawi. Ali kumeneko ankacheza kwambiri ndi amishonale omwe chitsanzo chawo chabwino chinamulimbikitsa kuti apitirizebe kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba.

Mu 2003, ine ndi Alex tinakwatirana ndipo kuyambira nthawi imeneyi takhala tikuchitira limodzi utumiki wanthawi zonse. Taphunzira zinthu zambiri zosangalatsa, ndipo Yehova watipatsa madalitso osawerengeka.

YEHOVA ANATIDALITSANSO KWAMBIRI

Vanessa ali mu utumiki limodzi ndi mlongo wachitsikana.

Tikulalikira m’tawuni ya Gleno, ku Timor-Leste

Mu 2009, tinatumizidwa kukatumikira monga amishonale m’dziko lina laling’ono lotchedwa Timor-Leste, limene ndi limodzi mwa zilumba za ku Indonesia. Titapatsidwa utumikiwu tinadabwa komanso tinachita mantha, koma tinasangalala kwambiri. Patapita miyezi 5 tinafika ku Dili lomwe ndi likulu la dzikoli.

Kukatumikira m’dzikoli kunachititsa kuti tisinthe zinthu zambiri pa moyo wathu. Tinafunika kuphunzira chikhalidwe, chilankhulo, chakudya komanso moyo watsopano. Nthawi zambiri tikalowa mu utumiki tinkakumana ndi anthu amene anali osauka kwambiri, osaphunzira komanso omwe ankaponderezedwa. Tinkaonanso anthu ambiri amene ankavutika maganizo komanso anali ndi zilema zobwera chifukwa cha nkhondo ndi ziwawa.a

Utumiki unkasangalatsa. Mwachitsanzo, nthawi ina ndinakumana ndi mtsikana wina wazaka 13, dzina lake Mariab yemwe sankasangalala. Panali patadutsa zaka zingapo kuchokera pamene mayi ake anamwalira ndipo ankangoonana mwa apo ndi apo ndi bambo ake. Mofanana ndi ana ambiri a msinkhu wake, Maria sankadziwa kuti adzachita chiyani pa moyo wake. Ndikukumbukira nthawi ina pamene analira kwambiri akundifotokozera mmene ankamvera. Koma sindinkamvetsa bwinobwino zonse zimene analankhula chifukwa ndinali ndisanadziwe bwino chilankhulo chake. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kupeza mfundo zimene zingamulimbikitse ndipo kenako ndinayamba kumuwerengera malemba otonthoza. Patapita zaka zochepa, ndinaona choonadi chikumuthandiza Maria kusintha zinthu pa moyo wake, mmene ankaonera zinthu komanso mmene ankaonekera. Iye anabatizidwa ndipo amachititsa maphunziro ake a Baibulo. Panopa Maria ali m’banja lauzimu la atumiki a Yehova ndipo amaona kuti amakondedwa.

Yehova akudalitsa ntchito yathu yolalikira ku Timor-Leste. Ngakhale kuti ofalitsa ambiri abatizidwa m’zaka 10 zapitazi, ambiri akutumikira monga apainiya, atumiki othandiza komanso akulu. Ena akutumikira m’maofesi omasulira mabuku ndipo akuthandiza kukonza chakudya chauzimu muzilankhulo zosiyanasiyana za m’dzikolo. Ndinkasangalala kwambiri kuwamva akuimba pamisonkhano, kuona nkhope zawo zachimwemwe komanso kuona kuti akulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.

Vanessa, Alex ndi abale atatu akomweko anayenda panjinga zamoto kuti akagawire timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso.

Ndili ndi Alex, tikupita kugawo lakutali kukagawa timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso

SINDIKANAPEZA MOYO WABWINO KUPOSA UMENEWU

Pamene tinkatumikira ku Timor-Leste zinthu zinali zosiyana kwambiri ndi ku Australia koma tinkasangalalabe moti ndimaona kuti sindikanapeza moyo wabwino kuposa umenewu. Nthawi zina tinkakwera maminibasi odzaza ndi anthu komanso atanyamula nsomba zouma ndi masamba zoti akagulitse kumsika. Masiku ena tinkachititsa maphunziro a Baibulo m’tinyumba ting’onoting’ono tomwe mkati mwake munkatentha komanso munkakhala mwakuda kwinaku tinkhuku tikuthamangathamanga. Ngakhale kuti tinkakumana ndi mavuto amenewa nthawi zambiri mumtimamu ndinkangoti, ‘Koma ndiye n’zosangalatsa bwanji.’

Vanessa, Alex ndi anthu ena akwera minibasi yodzadza ndi anthu ndipo abale atatu akwera ataimirira pakhomo pa minibasiyo.

Tili m’njira popita kugawolo

Ndikaganizira kale, ndimathokoza kwambiri makolo anga chifukwa choyesetsa kundiphunzitsa za Yehova komanso kundithandiza ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri ya unyamata. Zimene zinandichitikira zikusonyeza kuti lemba la Miyambo 22:6 ndi loona. Mayi anga ndi bambo anga amanyadira akaona ine ndi Alex ndipo amasangalala kwambiri kutiona tikutumikira Yehova. Kuchokera mu 2016 ine ndi Alex takhala tikuchita utumiki woyang’anira dera m’gawo la nthambi ya Australasia.

Ndikuonetsa mavidiyo a Kalebe ndi Sofiya kwa tiana tosangalala ta ku Timor-Leste

N’zovuta kukhulupirira kuti pa nthawi inayake sindinkasangalala ndi ntchito yolalikira. Koma panopa ndimakonda kwambiri utumiki. Ndazindikira kuti kaya tikumane ndi zotani pa moyo, chimwemwe chenicheni chimabwera chifukwa chotumikira Yehova ndi mtima wathu wonse. Kunena zoona, zaka 18 zimene ndakhala ndikutumikira limodzi ndi Alex, zakhala zaka zosangalatsa kwambiri pa moyo wanga. Tsopano ndimamvetsa mfundo ya choonadi imene wamasalimo Davide anauza Yehova kuti: “Onse othawira kwa inu adzakondwa. Adzafuula mokondwera mpaka kalekale. . . . Okonda dzina lanu adzakondwa chifukwa cha inu.”​—Sal. 5:11.

Vanessa ndi Alex ali panja pa nyumba ya mayi wina ndipo akuphunzira naye Baibulo limodzi ndi mwana wake.

Zimakhala zosangalatsa kuphunzira Baibulo ndi anthu odzichepetsa

a Kungoyambira mu 1975, ku Timor-Leste kunakhala kukuchitika nkhondo kwa zaka zoposa 20 chifukwa anthu ankafuna ufulu wodzilamulira.

b Dzina lasinthidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena