Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp22 No. 1 tsamba 3
  • N’zotheka Kuthetsa Chidani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’zotheka Kuthetsa Chidani
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Chidani Sichikutha?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Chidani Chikadzatheratu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
wp22 No. 1 tsamba 3
Zithunzi: Munthu wowawidwa mtima akuganizira zinthu zosiyanasiyana zachidani zomwe anthu akumuchitira komanso zomwe zikuulutsidwa pa TV. 1. Mzimayi yemwe ali ndi foni m’manja akumunyogodola momudelera. 2. Mzimayi wina akumuyang’ana momudelera. 3. Munthu yemwe akuwerenga nyuzipepala wamulusira ndipo wachita kumulumira mano. 4. Wofalitsa nkhani akuoneka pa TV.

N’zotheka Kuthetsa Chidani

Kodi munayamba mwadedwapo ndi anthu ena?

Ngati simunakumanepo ndi vuto limeneli n’kutheka kuti munaona anthu ena zikuwachitikira. Masiku ano nkhani zambiri zimakhala zokhudza kudana ndi anthu chifukwa cha mtundu wawo, dziko lomwe anachokera kapenanso chifukwa choti amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo. Chifukwa cha zimenezi maboma ambiri akumakhazikitsa malamulo n’cholinga choti amene wapezeka akudana ndi gulu linalake la anthu azipatsidwa chilango chokhwima.

Nthawi zambiri anthu amene amadedwa nawonso amayamba kudana ndi anthu ena. Anthu amene amadedwa amakonda kubwezera ndipo zimenezi zimachititsa kuti vutoli lizingopitirira.

N’kutheka kuti inuyo munakumanapo ndi zinthu monga kusalidwa, kunyozedwa chifukwa cha mtundu wanu, kunenedwa mawu achipongwe kapenanso kuopsezedwa. Komabe, chidani chimachititsa kuti anthu azichitirana zinthu zoopsa kwambiri monga nkhanza, kuwononga zinthu za ena, kugwiririra ngakhalenso kupha mwankhanza anthu amtundu winawake.

Magaziniyi isonyeza mmene tingathetsere chidani komanso iyankha mafunso otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani anthu amadana kwambiri?

  • N’chiyani chingathandize kuti anthu asiye kudana?

  • Kodi n’zotheka kuti chidani chidzatheretu padzikoli?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena