Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp22 No. 1 tsamba 6-7
  • 1 | Muziyesetsa Kupewa Tsankho

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 | Muziyesetsa Kupewa Tsankho
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo Limati:
  • Zimene Lembali Limatanthauza:
  • Mmene Lembali Lingakuthandizireni:
  • Tito—‘Wantchito Mnzanga Pokuthandizani’
    Nsanja ya Olonda—1998
  • 3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo Mwanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Tingathetse Bwanji Chidani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
wp22 No. 1 tsamba 6-7
Munthu wakuda wagwira chinthu za mzungu akumwetulira ndipo mzungu wagwira chithunzi cha munthu wakuda akumwetulira. Zithunzi zina zikusonyeza anthu olusa.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

1 | Muziyesetsa Kupewa Tsankho

Baibulo Limati:

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—MACHITIDWE 10:34, 35.

Zimene Lembali Limatanthauza:

Yehovaa Mulungu samatiweruza potengera mtundu wathu, mmene khungu lathu limaonekera kapenanso chikhalidwe chathu. Mulungu amaona zinthu zofunika kwambiri monga zomwe timaganiza komanso zimene timalakalaka mumtima mwathu. Baibulo limanenanso kuti munthu amaona zooneka ndi maso “koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”​—1 Samueli 16:7.

Mmene Lembali Lingakuthandizireni:

Ngakhale sitingadziwe zimene zili mumtima mwa munthu, tingatsanzire Mulungu pokhala anthu opanda tsankho. Muziyesetsa kuona munthu wina aliyense payekha m’malo momuweruza potengera mtundu wake. Ngati mukuona kuti muli ndi maganizo olakwika okhudza anthu ena chifukwa cha mtundu wawo, mungachite bwino kupemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kuthetsa maganizo amenewo. (Salimo 139:23, 24) Ngati mungapemphere kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kuti akuthandizeni kukhala opanda tsankho, iye adzayankha pemphero lanu ndipo adzakuthandizani.​—1 Petulo 3:12.

a Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.

“Ndinali ndisanakhalepo mwamtendere ndi mzungu . . . Tsopano zinali zotheka chifukwa ndili mu m’gulu la anthu okondana kwambiri lapadziko lonse.”​—TITUS

Zimene Zinachitikira Munthu Wina​—TITUS

Anasiya Kudana Ndi Anthu Amitundu Ina

Titus.

Titus anali m’gulu la zigawenga zolusa kwambiri zomwe zinkadana ndi malamulo okondera mtundu wina wa anthu. Iye anati: “Tinkapita kumalo osiyanasiyana kumene anthu akuda sankaloledwa kupitako, monga m’mahotela ndiponso malo omwera mowa, n’cholinga choti tikayambitse ndewu.” Iye akunena kuti ankachita zimenezi chifukwa chakuti anali ndi mtima wodana ndi anthu ena, ndipo anati: “Ndinkati ndikayambana ndi munthu wina, kaya akhale wamwamuna kapena wamkazi, nthawi zonse ineyo ndi amene ndinkakhala woyamba kuponya chibakera.”

Titus anayamba kusintha moyo wake atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Zimene anawerenga m’Baibulo, zinamuthandiza kusintha mmene ankaganizira. Iye anasangalala kwambiri atamva zimene Baibulo limalonjeza zokhudza dziko lapansi kuti “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Poyamba Titus ankavutika kuthetsa chidani mumtima mwake. Iye anati: “Zinali zovuta kuti ndisinthe mmene ndimaganizira ndiponso khalidwe langa.” Koma lemba la Machitidwe 10:34, 35, linamuthandiza kuzindikira kuti Mulungu alibe tsankho.

Ndiye zotsatirapo zake zinali zotani? Titus anafotokoza kuti: “Ndinakhulupirira kuti Mboni za Yehova zimalambira Mulungu moona nditaona kuti zimakondana mosayang’ana mtundu kapena khungu la munthu. Ndipo ngakhale ndisanabatizidwe munthu wina wa Mboni yemwe anali mzungu anandiitanira kunyumba kwake kuti ndikadye naye chakudya. Sindinakhulupirire zimenezi chifukwa ndinali ndisanakhalepo mwamtendere ndi mzungu ndipo sizikanatheka n’komwe kudya naye pamodzi. Tsopano zinali zotheka chifukwa ndili m’gulu la anthu okondana kwambiri lapadziko lonse.”

Werengani zambiri zokhudza mbiri ya moyo wa Titus mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2009, tsamba 28 ndi 29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena