Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp22 No. 1 tsamba 10-11
  • 3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo Mwanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo Mwanu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo Limati:
  • Zimene Lembali Limatanthauza:
  • Mmene Lembali Lingakuthandizireni:
  • “Sitefano Anali ndi Mphamvu Ndipo Ankachita Kuonekeratu Kuti Mulungu Ali Naye”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Stefano Aponyedwa Miyala
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi Tingathetse Bwanji Chidani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • N’zotheka Kuthetsa Chidani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
wp22 No. 1 tsamba 10-11
Munthu akuganizira akupatsana moni ndi munthu wina yemwe ndi wosiyana naye mtundu. Zithunzithunzi zawo zikusonyeza atanyamula zikwangwani za zionetsero komanso akukangana.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo Mwanu

Baibulo Limati:

“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—AROMA 12:2.

Zimene Lembali Limatanthauza:

Mulungu amadziwa bwino zimene timaganiza. (Yeremiya 17:10) Choncho pali zambiri zomwe tiyenera kuchita kuwonjezera pa kupewa kulankhula kapenanso kuchita zinthu zosonyeza kuti tili ndi mtima wachidani. Chidani chimayambira mumtima ndiponso m’maganizo athu ndiye n’chifukwa chake tiyenera kuthetseratu chidani mumtima komanso m’maganizo mwathu. Tikachita zimenezi m’pamenedi ‘tingasandulike’ komanso kuthetsa chidani.

Mmene Lembali Lingakuthandizireni:

Dzifufuzeni moona mtima kuti mudziwe mmene mumaonera anthu ena, makamaka amitundu ina. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimawaona bwanji? Kodi ndimawaona chonchi chifukwa chakuti ndimawadziwa bwino kapena chifukwa choti ndili ndi mtima watsankho?’ Muzipewa mafilimu, kuwerenga kapena kuonera zinthu za pa intaneti ndiponso zosangalatsa zomwe zimalimbikitsa chidani komanso zachiwawa.

Mawu a Mulungu angatithandize kuthetsa chidani mumtima ndi m’maganizo mwathu

Si zophweka kudzifufuza moona mtima ndi cholinga choti tidziwe ngati tili ndi maganizo olakwika. Koma Mawu a Mulungu angatithandize kuti tithe kuzindikira zomwe ‘tikuganiza komanso zolinga za mtima wathu.’ (Aheberi 4:12) Choncho, musasiye kufufuza mfundo za m’Baibulo. Muziyerekezera zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zimene mumaganiza kenako muziyesetsa kusintha maganizo anu kuti agwirizane ndi zimene mukuphunzira m’Baibulo. Mawu a Mulungu angatithandize kuthetsa chidani chimene ‘chinazikika molimba’ m’maganizo komanso mumtima mwathu.​—2 Akorinto 10:4, 5.

Zimene Zinachitikira Munthu Wina​—STEPHEN

Anasintha Mmene Ankaganizira

Stephen.

Stephen ndi anthu am’banja lake ankadedwa ndi azungu. Mapeto ake analowa gulu linalake landale limene linkamenyera ufulu wa anthu. Patapita nthawi, Stephen anayamba kudana ndi anthu amitundu ina n’kumawachitira nkhanza. Iye anati: “Nthawi ina ndili ndi anzanga tinaonera filimu yosonyeza mmene akapolo a ku Africa anazunzidwira ku United States. Zimenezi zinatikwiyitsa kwambiri moti nthawi yomweyo tinayamba kumenya azungu achinyamata amene ankaonera nawo filimuyo. Kenako tinayamba kusakasaka m’nyumba za anthu oyandikana nawo kuti tikapeza azungu tiziwamenya.”

Stephen atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova anasinthiratu mmene ankaganizira. Iye anati: “Popeza ndinakula ndi moyo watsankho, ndinkachita chidwi kwambiri ndi zimene a Mboni ankachita. Mwachitsanzo, mzungu wina wa Mboni anasiira ana ake banja lina lachikuda pa nthawi imene ankachoka. Komanso banja lina lachizungu linkakhala ndi mnyamata wachikuda yemwe ankasowa pokhala.” Stephen anaona kuti a Mboni za Yehova ali ngati banja la anthu okondana ndipo zimenezi zinamuthandiza kumvetsa bwino zimene Yesu ananeneratu kuti Akhristu oona azidzasonyezana chikondi chenicheni.​—Yohane 13:35.

N’chiyani chinathandiza Stephen kuti asiye khalidwe lachiwawa komanso lodana ndi anthu ena? Lemba lomwe linamuthandiza kwambiri ndi la Aroma 12:2. Iye anati: “Ndinazindikira kuti ndikufunika kusintha mmene ndimaganizira. Ndinafunika kusintha maganizo anga kuti ndizichita zinthu mwamtendere komanso kuona kuti kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri pa moyo wanga.” Kwa zaka 40 tsopano, Stephen akukhala moyo wosangalala chifukwa anasiya kudana ndi anthu.

Kuti mumve zambiri zokhudza mbiri ya moyo wa Stephen, werengani magazini ya Nsanja ya Olonda ya July 1, 2015, tsamba 10 ndi 11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena