Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp22 No. 1 tsamba 12-13
  • 4 | Mulungu Angakuthandizeni Kuthetsa Mtima Wachidani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 4 | Mulungu Angakuthandizeni Kuthetsa Mtima Wachidani
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo Limati:
  • Zimene Lembali Limatanthauza:
  • Mmene Lembali Lingakuthandizireni:
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Tingathetse Bwanji Chidani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • N’zotheka Kuthetsa Chidani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • N’chifukwa Chiyani Chidani Sichikutha?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
wp22 No. 1 tsamba 12-13
Anthu akuyenda kulowera kumene kuli Baibulo lalikulu lotsegula lomwe likuwaunika. Zithunzithunzi zawo zikuimira chidani chawo chakale.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

4 | Mulungu Angakuthandizeni Kuthetsa Mtima Wachidani

Baibulo Limati:

“Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”​—AGALATIYA 5:22, 23.

Zimene Lembali Limatanthauza:

Mulungu angatithandize kuthetsa chidani. Mzimu wake woyera ungatithandize kukhala ndi makhalidwe amene patokha sitingakwanitse kukhala nawo. Choncho, m’malo moyesetsa kulimbana ndi kuthetsa mtima wachidani patokha, tingachite bwino kudalira Mulungu kuti atithandize. Tikachita zimenezi tidzafanana ndi Paulo yemwe analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Komanso tidzanena kuti: “Thandizo langa lichokera kwa Yehova.”​—Salimo 121:2.

Mmene Lembali Lingakuthandizireni:

“Yehova wandithandiza kuti ndisinthe khalidwe langa lokonda zachiwawa moti panopa ndine munthu wokonda mtendere.”—WALDO

Muzipemphera kwa Yehova moona mtima kuti akupatseni mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Muzimupempha kuti akuthandizeni kukhala ndi makhalidwe abwino. Muziphunzira Baibulo kuti mudziwe makhalidwe amene angakuthandizeni kuthetsa chidani monga chikondi, mtendere, kuleza mtima ndi kudziletsa. Muziyesetsa kuganizira zimene mungachite kuti mukhale ndi makhalidwe amenewa pa moyo wanu. Ndiponso muzicheza ndi anthu omwe akuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amenewa. Anzanu oterewa ‘adzakulimbikitsani pa chikondi ndi ntchito zabwino.’​—Aheberi 10:24.

Zimene Zinachitikira Munthu Wina​—WALDO

Anasiya Kudana Ndi Anthu Ena Komanso Kuchita Zachiwawa

Waldo.

Waldo ali wamng’ono anakumana ndi mavuto ambiri omwe anamuchititsa kuti ayambe kudana ndi anthu ena. Iye anati: “Nthawi zambiri ndinkamenyana ndi anthu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo . . . Pa nthawi ina gulu lina la zigawenga limene tinkalimbana nalo kwambiri, linalemba ganyu chigawenga choopsa kwambiri n’cholinga choti chindiphe koma mwamwayi ndinakwanitsa kuthawa atandibaya ndi mpeni.”

Waldo sanasangalale ataona kuti mkazi wake wayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Iye anati: “Ndinkadana ndi a Mboni ndipo nthawi zambiri ndinkawatukwana. Koma ndinkadabwa nawo chifukwa sankandibwezera.”

Patapita nthawi nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Iye anati: “Zinkandivuta kuti ndizigwiritsa ntchito zimene ndinkaphunzira. Ndinkaona kuti n’zosatheka kusiya khalidwe langa lankhanza.” Koma mfundo ina imene anaphunzira m’Baibulo inamuthandiza kusintha maganizo amenewa.

Waldo anafotokoza kuti: “Tsiku lina m’bale amene ankandiphunzitsa Baibulo, dzina lake Alejandro, anandiuza kuti ndiwerenge Agalatiya 5:22, 23. . . . Alejandro anandiuza kuti sindingakhale ndi makhalidwe amenewa pandekha, ndikufunika kudalira mzimu woyera wa Mulungu. Mfundo imeneyi inandithandiza kusintha maganizo amene ndinali nawo.”

Waldo anakwanitsa kusiya kudana ndi anthu ena chifukwa chakuti anadalira Mulungu kuti amuthandize. Iye anati: “Abale anga komanso anzanga samamvetsa akaona kuti ndinasintha.” Iye ananenanso kuti: “Yehova wandithandiza kuti ndisinthe khalidwe langa lokonda zachiwawa moti panopa ndine munthu wokonda mtendere.”

Kuti mumve zambiri zokhudza mbiri ya moyo wa Waldo, werengani magazini ya Nsanja ya Olonda ya October 1, 2013, tsamba 12 ndi 13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena