Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w22 December tsamba 22-27
  • Muzithandiza Ena Kupirira pa Nthawi Zovuta

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Ena Kupirira pa Nthawi Zovuta
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MUZITHANDIZA ENA KUKAGWA MLIRI
  • TIZITHANDIZA OMWE AKHUDZIDWA NDI NGOZI YAM’CHILENGEDWE
  • TIZITHANDIZA ABALE ATHU KUPIRIRA AKAMAZUNZIDWA
  • Mungathe Kupeza Mtendere pa Nthawi ya Mavuto
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Akulu, Pitirizani Kutsanzira Mtumwi Paulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Mwakonzekera Masoka Achilengedwe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Mpingo wa Chikhristu Umayendetsedwa bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
w22 December tsamba 22-27

NKHANI YOPHUNZIRA 52

Muzithandiza Ena Kupirira pa Nthawi Zovuta

“Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.”​—MIY. 3:27.

NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso za Amuna

ZIMENE TIPHUNZIREa

1. Kodi nthawi zambiri Yehova amayankha bwanji mapemphero a atumiki ake?

KODI mukudziwa kuti Yehova akhoza kugwiritsa ntchito inuyo poyankha pemphero lochokera pansi pa mtima la munthu wina? Iye angakugwiritseni ntchito kaya ndinu mkulu, mtumiki wothandiza, mpainiya kapenanso wofalitsa. Angakugwiritseni ntchito kaya ndinu wamng’ono kapena wamkulu ndiponso kaya ndinu m’bale kapena mlongo. Munthu amene amakonda Yehova akamupempha kuti amuthandize, Mulungu angagwiritse ntchito mkulu kapena mtumiki wake wokhulupirika aliyense kuti ‘amuthandize ndi kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:11) Ndi mwayitu waukulu kutumikira Yehova komanso abale athu m’njira imeneyi. Tingathe kuchita zimenezi pa nthawi imene kwagwa mliri, kwachitika ngozi yam’chilengedwe kapenanso pamene tikuzunzidwa.

MUZITHANDIZA ENA KUKAGWA MLIRI

2. N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuthandiza ena kukagwa mliri?

2 Zingakhale zovuta kuti tizithandizana kukagwa mliri. Mwachitsanzo, mwina tingafune kukacheza kwa anzathu koma zingakhale zoopsa kuchita zimenezi. Mwinanso tingafune kuitanira chakudya anzathu omwe akukumana ndi mavuto azachuma koma zimenezinso zingakhale zosatheka. Tingafune kuthandiza ena koma zingakhale zovuta ngati anthu am’banja lathunso akuvutika. Komabe timafuna kuthandiza abale athu chifukwa Yehova amasangalala tikachita zomwe tingathe powathandiza. (Miy. 3:27; 19:17) Ndiye kodi tingawathandize bwanji?

3. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha akulu a mumpingo wa Desi? (Yeremiya 23:4)

3 Zimene akulu angachite. Ngati ndinu mkulu, muzidziwa bwino nkhosa. (Werengani Yeremiya 23:4.) Desi, mlongo yemwe tamutchula munkhani yapita ija anati: “Akulu a m’kagulu kathu ankalowa nafe mu utumiki komanso tinkakhala nawo limodzi pakakhala macheza.”b Zimenezi zinathandiza akuluwa kuti asavutike kuthandiza Desi pa nthawi ya mliri wa COVID-19 pamene anthu a m’banja lake ena anamwalira ndi mliriwu.

4. N’chifukwa chiyani akulu anakwanitsa kuthandiza Desi, nanga tikuphunzirapo chiyani?

4 Desi anafotokoza kuti: “Popeza ndinkadziwa kuti akuluwo ndi anzanga, sizinandivute kuwafotokozera mmene ndinkamvera komanso zimene zinkandidetsa nkhawa.” Kodi akulu angaphunzirepo chiyani? Muzisamalira anthu amene ndi udindo wanu kuwasamalira mavuto asanabwere. Muzikhala anzawo. Ngati kwagwa mliri womwe ukukulepheretsani kuti muwayendere, muziwathandiza m’njira zina. Desi anati: “Nthawi zina, pa tsiku limodzi akulu angapo ankandiimbira foni kapena kunditumizira mameseji. Malemba omwe ankandiwerengera ankandifika pamtima ngakhale kuti ndinkawadziwa kale.”

5. Kodi akulu angadziwe bwanji zimene abale ndi alongo akufunikira, nanga angawathandize bwanji?

5 Njira imodzi imene mungadziwire zimene abale ndi alongo anu akufunikira ndi kuwafunsa mafunso mwanzeru. (Miy. 20:5) Kodi ali ndi chakudya chokwanira, mankhwala kapena zinthu zina zofunika? Kodi akhoza kuchotsedwa ntchito kapenanso kutulutsidwa m’nyumba imene akukhala? Kodi akufunika kuwathandiza mmene angapemphere thandizo ku boma? Desi anapatsidwa zimene ankafunikira ndi Akhristu anzake. Koma chomwe chinamuthandiza kupirira mavuto ake ndi kulimbikitsidwa komanso kuthandizidwa mwauzimu ndi akulu. Iye anati: “Akulu ankapemphera nane. Ngakhale kuti sindingakumbukire bwinobwino zomwe ankanena, ndimakumbukira mmene ndinkamvera. Ndi njira imene Yehova ankandiuzira kuti, ‘Suli wekha.’”​—Yes. 41:10, 13.

Zithunzi: 1. M’bale akuchititsa misonkhano pamasom’pamaso ku Nyumba ya Ufumu. Akugwiritsa ntchito tabuleti kuti azitha kuona m’bale yemwe akudwala ndipo walumikizidwa pa vidiyokomfelensi. 2. M’bale yemwe akuchita nawo misonkhano ali kunyumba akuimika dzanja kuti apereke ndemanga. Iye ali pa okosijeni.

M’bale yemwe akuchititsa Nsanja ya Olonda akusangalala ndi ndemanga zolimbikitsa za onse omwe apezeka pamisonkhano kuphatikizaponso m’bale yemwe akudwala ndipo walumikizidwa kudzera pa vidiyokomfelensi (Onani ndime 6)

6. Kodi ambiri angachite chiyani mumpingo pothandiza ena? (Onani chithunzi.)

6 Zimene ena angachite. Timayembekezera kuti akulu ndi amene angatsogolere pothandiza ena. Koma Yehova amatipempha kuti tonsefe tizilimbikitsa komanso kuthandiza ena. (Agal. 6:10) Ngakhale zochepa zomwe tingachite posonyeza chikondi kwa munthu yemwe akudwala, zingamulimbikitse kwambiri. Mwana akhoza kutumiza khadi kapena kujambula chithunzi pofuna kulimbikitsa m’bale. Wachinyamata angathandize pa ntchito zina kapena kukagulira zinthu mlongo. Tingathenso kukonza chakudya n’kukapereka kwa munthu yemwe akudwala. Komabe pa nthawi imene kwagwa mliri, aliyense mumpingo amafunika kulimbikitsidwa. Mwinanso tingatsalire pambuyo pa misonkhano kuti ticheze ndi abale ndi alongo kaya pamasom’pamaso kapena kudzera pa vidiyokomfelensi. Nawonso akulu amafunika kulimbikitsidwa. A Mboni ena amatumiza kakhadi kothokoza kwa akulu omwe amakhala otanganidwa kwambiri pa nthawi ya mliri. Ndi bwinotu kuti tizichita mbali yathu popitiriza “kutonthozana ndi kulimbikitsana.”​—1 Ates. 5:11.

TIZITHANDIZA OMWE AKHUDZIDWA NDI NGOZI YAM’CHILENGEDWE

7. Kodi ngozi yam’chilengedwe ikachitika pangakhale mavuto otani?

7 Ngozi yam’chilengedwe ingasinthe kwambiri moyo wa munthu mosayembekezereka. Anthu ena angataye katundu, nyumba kapena anthu omwe ankawakonda. Zoopsa ngati zimenezi zingachitikirenso abale ndi alongo athu. Ndiye kodi tingawathandize bwanji?

8. Kodi akulu ndi mitu ya mabanja angachite chiyani ngozi isanachitike?

8 Zimene akulu angachite. Akulu, muzithandiza abale anu kukhala okonzeka ngozi isanachitike. Muzionetsetsa kuti onse mumpingo akudziwa zomwe angachite kuti akhale otetezeka komanso kuti azilankhulana ndi akulu. Margaret yemwe tamutchula munkhani yapita ija ananena kuti: “Akulu anakamba nkhani ya zofunika pampingo ndipo anatichenjeza kuti moto wolusa ukhoza kuyambanso. Iwo ananena kuti ngati akuluakulu a boma atatilamula kuti tichoke, kapena tikaona kuti zinthu sizili bwino tiyenera kuchoka mwamsanga.” Amenewatu anali malangizo a pa nthawi yake chifukwa patangodutsa milungu 5, moto wolusa kwambiri unayamba. Pa kulambira kwa pabanja mitu ya mabanja ingakambirane ndi anthu a m’banja lawo zimene aliyense angachite pa nthawi ya ngozi. Ngati inuyo ndi ana anu mwakonzekera, simungapanikizike kwambiri ngozi ikachitika.

9. Kodi akulu angachite chiyani ngozi yam’chilengedwe isanachitike komanso pambuyo pake?

9 Ngati ndinu woyang’anira kagulu ka utumiki, muzionetsetsa kuti muli ndi ma adiresi ndi manambala a foni olondola a anthu a m’kagulu kanu ndipo muzichita zimenezi ngozi isanachitike. Muzilemba zimenezi penapake ndipo nthawi ndi nthawi muzitsimikizira kuti ndi zolondola. Ndiyeno ngozi ikachitika, mungathe kulankhula ndi wofalitsa aliyense kuti mudziwe zimene akufunikira. Mwamsanga muziuza zimenezo wogwirizanitsa ntchito za akulu yemwe adzalumikizana ndi woyang’anira dera. Kuchita zinthu mogwirizana kwa abalewa kungathandize kwambiri. Moto utayaka m’dera limene Margaret ankakhala, woyang’anira dera sanagone kwa maola 36 ndipo ankagwira ntchito ndi akulu kuti asamalire abale ndi alongo 450 omwe anathawa m’nyumba zawo. (2 Akor. 11:27) Choncho onse omwe ankafunika malo okhala, anapatsidwa pokhala.

10. N’chifukwa chiyani akulu amaona kuti kulimbikitsa ena pogwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba n’kofunika? (Yohane 21:15)

10 Imodzi mwa ntchito zimene akulu amagwira ndi kulimbikitsa abale ndi alongo awo ndi mfundo za m’Baibulo komanso kuwathandiza kuti asakhale ndi nkhawa. (1 Pet. 5:2) Pakachitika ngozi, choyamba akulu amaonetsetsa kuti aliyense ali ndi chakudya, zovala komanso pokhala. Komabe kwa miyezi yambiri pambuyo pa ngoziyo opulumukawo angafunike kupitirizabe kulimbikitsidwa ndi mfundo za m’Malemba. (Werengani Yohane 21:15.) Harold, yemwe amatumikira m’Komiti ya Nthambi, ndipo anakumanapo ndi abale ndi alongo ambiri omwe anakhudzidwa ndi ngozi ananena kuti: “Pamatenga nthawi kuti munthu ayambirenso kuchita zinthu ngati kale. Iwo angayambe kuiwala za zinthu zimene anataya komabe zingawavute kuiwala imfa ya okondedwa awo, zinthu zawo zamtengo wapatali komanso mmene zinalili zovuta kuti apulumuke. Akamakumbukira zinthu ngati zimenezi, angayambirenso kukhala ndi chisoni. Zimenezi sizitanthauza kuti munthu alibe chikhulupiriro. Koma ndi mmene munthu aliyense angamvere mwachibadwa.”

11. Kodi mabanja angafunikirebe chiyani?

11 Akulu amatsatira malangizo akuti “lirani ndi anthu amene akulira.” (Aroma 12:15) Anthu omwe apulumuka ngozi angafunike kuwatsimikizira kuti Yehova komanso Akhristu anzawo sanasiye kuwakonda. Akulu amafuna kuthandiza mabanja kupitirizabe kuchita zinthu zokhudza kulambira monga kupemphera, kuphunzira, kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira. Akulu angalimbikitsenso makolo kuti azithandiza ana awo kuti aziganizira kwambiri zinthu zimene sizingawonongedwe ndi ngozi iliyonse. Makolo, muzikumbutsa ana anu kuti nthawi zonse Yehova adzakhala Mnzawo ndipo adzawathandiza. Ndiponso muziwafotokozera kuti nthawi zonse adzakhalabe m’banja lapadziko lonse la abale ndi alongo omwe ndi okonzeka kuwathandiza.​—1 Pet. 2:17.

Banja likupereka madzi ndi zinthu zina kwa mayi ndi mwana wake omwe ali mu tenti.

Kodi mungadzipereke kuti muthandize pamene kwachitika ngozi inayake m’dera lanu? (Onani ndime 12)e

12. Kodi ena angachite chiyani kuti athandize pamene kwachitika ngozi? (Onani chithunzi.)

12 Zimene ena angachite. Ngati ngozi yachitika pafupi ndi dera lanu, muzifunsa akulu mmene mungathandizire. Mwina mungalandire m’nyumba yanu anthu omwe alibe pokhala kapenanso amene adzipereka kugwira ntchito zomangamanga. Mungathandizenso pokapereka chakudya ndi zinthu zina zofunika kwa ofalitsa omwe akufunika thandizo. Mungathenso kuthandiza ngakhale ngozi itachitika kutali ndi kumene mumakhala. Motani? Popempherera amene akhudzidwa. (2 Akor. 1:8-11) Mungathandizenso popereka ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. (2 Akor. 8:2-5) Ngati mungakwanitse kupita kumene kwachitika ngozi, mungafunse akulu kuti akuuzeni zimene mungachite kuti mukathandize nawo. Ngati mwaitanidwa kuti mukathandize, mudzapatsidwa maphunziro amene angakuthandizeni kuti mukhale oyenerera kukathandiza.

TIZITHANDIZA ABALE ATHU KUPIRIRA AKAMAZUNZIDWA

13. Kodi abale athu amakumana ndi mavuto otani m’mayiko omwe ntchito yathu ndi yoletsedwa?

13 M’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa, kuzunzidwa kumachititsa kuti moyo ukhale wovuta kwambiri kwa abale athu. Iwo amakumananso ndi mavuto azachuma, matenda komanso imfa ya anthu amene amawakonda. Chifukwa choti ntchito yathu ndi yoletsedwa, zingamawavutenso akulu kuti aziyendera komanso kulankhulana ndi anthu amene akufunika kulimbikitsidwa. Umu ndi mmenenso zinalili ndi Andrei yemwe tamutchula munkhani yapita ija. Mlongo wina wa m’kagulu kake ka utumiki ankakumana ndi mavuto azachuma. Kenako anachita ngozi ya galimoto. Ankafunika kuchitidwa maopaleshoni ambiri ndipo sankagwiranso ntchito. Ngakhale kuti ntchito yathu inali yoletsedwa komanso panali mliri, abale ndi alongo anayesetsa kuchita zonse zomwe akanatha kuti athandizepo, ndipo Yehova ankadziwa zimene zinkachitika.

14. Kodi akulu angatani kuti akhale chitsanzo chabwino pa nkhani yodalira Yehova?

14 Zimene akulu angachite. Andrei anapemphera ndipo anachita zomwe akanakwanitsa. Kodi Yehova anayankha bwanji pemphero lake? Iye anachititsa kuti abale ndi alongo ena, omwe akanatha kuyenda mosavuta akathandize mlongoyo. Ena ankamutenga mlongoyo popita naye kuchipatala. Ena ankamuthandiza ndi ndalama. Yehova anachititsa kuti iwo achite zomwe akanakwanitsa, ndipo anadalitsa zonse zomwe ankachita. (Aheb. 13:16) Akulu, ngati ntchito yathu yaletsedwa muzipempha thandizo kwa ena. (Yer. 36:5, 6) Koposa zonse, muzidalira Yehova. Iye angakuthandizeni kuti muthe kusamalira abale ndi alongo athu.

15. Kodi tingatani kuti tipitirizebe kukhala ogwirizana tikamazunzidwa?

15 Zimene ena angachite. Pamene ntchito yathu yaletsedwa, tingafunike kumasonkhana m’timagulu ting’onoting’ono. Choncho n’zofunika kwambiri kuti panopa tizikhala mwamtendere. Tizilimbana ndi Satana osati tokhatokha. Tizinyalanyaza zimene abale athu amalakwitsa kapena tiziyesetsa kuthetsa mwamsanga kusemphana maganizo kulikonse. (Miy. 19:11; Aef. 4:26) Tizikhala okonzeka kuthandizana. (Tito 3:14) Zimene ena m’kagulu ka utumiki kaja anachita pothandiza mlongo uja, zinathandiza kwambiri kagulu konseko. Iwo anakhala ogwirizana kwambiri ngati anthu a m’banja limodzi.​—Sal. 133:1.

16. Mogwirizana ndi Akolose 4:3, 18, kodi tingathandize bwanji abale ndi alongo athu omwe akuzunzidwa?

16 Abale ndi alongo athu ambiri akupitirizabe kutumikira Yehova ngakhale kuti ali m’mayiko amene boma linaletsa ntchito yathu. Ena anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Tingapempherere abalewa, mabanja awo komanso anthu amene amaika moyo wawo pangozi kuti akalimbikitse abale ndi alongo amenewa ndi mfundo za m’Malemba, kuwapatsa zofunika pa moyo komanso kukawaimira m’makhoti.c (Werengani Akolose 4:3, 18.) Musamaiwale kuti mapemphero anu angathandize kwambiri abale ndi alongo amenewa.​—2 Ates. 3:1, 2; 1 Tim. 2:1, 2.

Bambo, mkazi ndi ana ake akuchita kulambira kwa pabanja. Mwana wamng’ono akufotokoza zomwe waphunzira muvidiyo yakuti “Danieli Anali Munthu Wachikhulupiriro Cholimba.”

Kodi mungakonzekeretse bwanji anthu a m’banja lanu kudziwa zochita pamene akuzunzidwa? (Onani ndime 17)

17. Kodi panopa mungakonzekere bwanji kuzunzidwa?

17 Panopa inuyo ndi banja lanu mungakonzekereretu zimene mungachite pa nthawi imene mukuzunzidwa. (Mac. 14:22) Musamayese kuganizira zinthu zonse zoipa zomwe zingachitike. M’malomwake, muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova ndipo muzithandizanso ana anu kuchita zomwezo. Ngati nthawi zina mumayamba kukhala ndi nkhawa, muzimuuza Mulungu za mumtima mwanu. (Sal. 62:7, 8) Monga banja, muzikambirana zifukwa zomwe zingakuchititseni kuti muzimukhulupirira.d Monga mmene mumakonzekerera ngozi zosiyanasiyana, kukonzekera zimene mungachite mukamazunzidwa komanso kukhulupirira Yehova, kungathandize ana anu kukhala ndi mtendere komanso olimba mtima.

18. Kodi tikuyembekezera chiyani m’tsogolo?

18 Mtendere wa Mulungu umatithandiza kudzimva kuti ndife otetezeka. (Afil. 4:6, 7) Ngakhale kuti masiku ano tingakumane ndi mavuto monga matenda, ngozi zam’chilengedwe kapena kuzunzidwa mtenderewu umathandiza kuti mitima yathu ikhale m’malo. Mulungu amagwiritsa ntchito akulu akhama kuti azitilimbikitsa. Watipatsanso mwayi tonsefe woti tizithandizana. Panopa pamene tili pa mtendere, ndi nthawi yabwino yomwe tingakonzekere mavuto aakulu omwe tingakumane nawo m’tsogolo, ngakhalenso “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21) Pa nthawiyo, tidzafunika kupitirizabe kukhala ndi mtendere komanso kuthandiza ena kuti nawonso akhale ndi mtendere. Pambuyo pa chisautso chachikulu, sitidzakumananso ndi mavuto alionse otidetsa nkhawa. Tidzasangalala monga mmene Yehova wakhala akufunira nthawi zonse ndi mtendere weniweni womwe sudzatha.​—Yes. 26:3, 4.

KODI TINGATHANDIZE BWANJI ENA KUPEZA MTENDERE PAMENE . . .

  • kwagwa mliri?

  • kwachitika ngozi zam’chilengedwe?

  • akuzunzidwa?

NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima

a Nthawi zambiri Yehova amagwiritsa ntchito atumiki ake okhulupirika pothandiza amene akukumana ndi mavuto. Angagwiritsenso ntchito inuyo polimbikitsa abale ndi alongo anu. Tiyeni tione mmene tingathandizire ena akakhala pa mavuto.

b Mayina ena asinthidwa.

c N’zosatheka kuti ofesi ya nthambi kapena abale ku likulu lathu la padziko lonse azitumiza makalata ochokera kwa anthu kwa abale ndi alongo omwe ali m’ndende.

d Onani nkhani yakuti, “Tizikonzekera Kuti Tidzathe Kupirira Pozunzidwa” mu Nsanja ya Olonda ya July 2019.

e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale ndi mkazi wake akupereka chakudya kwa banja lina lomwe lilibe pokhala pambuyo pa ngozi yam’chilengedwe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena