Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 8
  • Kodi Mwakonzekera Masoka Achilengedwe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwakonzekera Masoka Achilengedwe?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakonzekera?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Muzithandiza Ena Kupirira pa Nthawi Zovuta
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhondo ya Munthu ndi Masoka
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 8

Kodi Mwakonzekera Masoka Achilengedwe?

1. N’chifukwa chiyani chili chinthu chanzeru kukhala okonzekereratu masoka?

1 Chaka chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi, kuphatikizapo abale ndi alongo athu ambiri, amakhudzidwa ndi zivomezi, kusefukira kwa nyanja zazikulu kotchedwa tsunami, mvula ya mkuntho, kavulumvulu, ndi madzi osefukira. Popeza kuti masoka achilengedwewa amangochitika mosayembekezereka ndipo angakhudze aliyense wa ife, tingachite bwino kukhala okonzekeratu.—Miy. 21:5.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwitsa akulu za kumene tikukhala tsopano ndiponso nambala yathu ya telefoni?

2 Pasadakhale: Nthawi zina boma limatha kuchenjeza za masoka amene akubwera. Ndi bwino kumvera machenjezo amenewo. (Miy. 22:3) Zikatero, akulu aziyesetsa kuuza anthu onse a mumpingo powathandiza kukonzekera moyenerera. Pambuyo pa tsokalo, akulu adzayesetsanso kulankhulana ndi anthu onse omwe amasonkhana mumpingomo kuti aone ngati sanavulale ndiponso kuti adziwe thandizo limene akufunikira. Nthawi yambiri ingawonongeke ngati akuluwo alibe njira yabwino yodziwira za anthuwo. Choncho n’kofunika kuti wofalitsa aliyense adziwitse mlembi ndiponso woyang’anira phunziro la buku, za kumene akukhala kapena za nambala yake ya telefoni.

3. Kodi tingagwirizane bwanji ndi akulu ngati tikukhala m’dera limene kumachitikachitika masoka?

3 Ngati mpingo uli m’dera limene kumachitikachitika masoka, akulu angafunse ofalitsa kuti apereke dzina ndi nambala ya telefoni ya wachibale wawo kapena mnzawo amene sakhala m’dera limenelo, ndiponso amene angadziwitsidwe ngati kutachitika zinthu zamwadzidzidzi. Zimenezi zingathandize akulu kuti adziwe anthu amene asamutsidwa. Akulu angafunenso kukonza mapulani odalirika a mmene mpingo ungachitire pakaoneka tsoka, amene angaphatikizepo zinthu monga ndondomeko yachidule ya zinthu zimene aliyense ayenera kukhala nazo, mmene angasamukire, ndiponso mmene angathandizire anthu amene akufunika thandizo lapadera. Kugwirizana ndi makonzedwe achikondi amenewa, n’kofunika.—Aheb. 13:17.

4. Kodi tingachite chiyani ngati m’dera lathu mwachitika tsoka?

4 Pambuyo Pake: Kodi mungatani ngati m’dera lanu mwachitika tsoka? Onetsetsani kuti banja lanu lili ndi zinthu zakuthupi zofunikira panthawiyo. Ngati mungathe, thandizaninso anthu ena amene akhudzidwa ndi tsokalo. Yesetsani kulankhulana ndi woyang’anira phunziro la buku lanu kapena mkulu wina mwamsanga. Muyenera kutero ngakhale musanavulale ndipo simukufunikira thandizo. Ngati mukufunikira thandizo, musakayike kuti abale anu akuchita chilichonse chotheka kuti akuthandizeni. (1 Akor. 13:4, 7) Kumbukirani kuti Yehova akudziwa mavuto anu; dalirani iye ndipo adzakuchirikizani. (Sal. 37:39; 62:8) Khalani tcheru kupezerapo mwayi wolimbikitsa ena mwakuthupi ndiponso mwauzimu. (2 Akor. 1:3, 4) Yambiraninso mwamsanga kuchita zinthu zauzimu.—Mat. 6:33.

5. Kodi Akhristufe timakhudzidwa motani ndi nkhani zoti kuchitika tsoka?

5 Anthu padzikoli akuda nkhawa poganizira za masoka, koma ife sitikayikira kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Posachedwapa masoka onse adzakhala mbiri yakale. (Chiv. 21:4) Koma pa nthawi ino, tichite zonse zimene tingathe pokonzekera masoka ndi zovuta kwinaku tikupitirizabe kukhala achangu polengeza uthenga wabwino kwa ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena