MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mwakonzekera?
Ngati m’dera lanu mutachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, kodi ndinu wokonzeka? Zivomezi, mphepo zamkuntho, moto wa m’nkhalango, komanso madzi osefukira zikhoza kuchitika mwadzidzidzi ndipo zikhoza kuwononga zinthu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, zauchigawenga, zipolowe, komanso miliri zikhoza kuchitika kwina kulikonse mosayembekezeka. (Mlal. 9:11) Tisamaganize kuti zinthu ngati zimenezi sizingachitike m’dera limene tikukhala.
Aliyense ayenera kuchita zinazake pokonzekera ngozi zogwa mwadzidzidzi. (Miy. 22:3) Ngakhale kuti gulu la Yehova limapereka chithandizo pakachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, zimenezi sizikutanthauza kuti patokha tilibe udindo wochitapo kanthu.—Agal. 6:5.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGACHITE POKONZEKERA MASOKA ACHILENGEDWE NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi tingakonzekere bwanji mwauzimu masoka asanachitike?
N’chifukwa chiyani muyenera . . .
• kumalankhulana ndi akulu tsoka lisanachitike, likamachitika, komanso pambuyo poti lachitika?
• kukhala ndi zinthu zomwe mungazigwiritse ntchito pakachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi?—g17.5 6
• kukambirana mitundu ya masoka omwe angachitike komanso zimene mungachite masokawo akachitika?
Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tingachite pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi tsoka linalake?