Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp23 No. 1 tsamba 8-9
  • 2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’
  • sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tanthauzo Lake
  • Mmene Mfundo Zimenezi Zingakuthandizireni
  • N’chifukwa Chiyani Achinyamata Ambiri Akudwala Matenda Ovutika Maganizo?
    Galamukani!—2017
  • “Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amathandiza
    Galamukani!—2009
  • Kupsinjika Mtima Kodi Kungalakidwe Motani?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Mungatani Kuti Musamangokhala Wankhawa Ndiponso Wachisoni?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
wp23 No. 1 tsamba 8-9
Bambo wachikulire akuganizira zimene akuwerenga m’Baibulo.

2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’

BAIBULO LIMATI: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—AROMA 15:4

Tanthauzo Lake

M’Baibulo muli mfundo zolimbikitsa zimene zingatipatse mphamvu komanso kutithandiza kupirira kuti tithane ndi maganizo olakwika. Baibulo limatipatsanso chiyembekezo chakuti kuvutika maganizo kulikonse kudzatha.

Mmene Mfundo Zimenezi Zingakuthandizireni

Nthawi zina tonsefe timakhala ndi nkhawa koma anthu amene amavutika ndi matenda amaganizo kapena nkhawa, tsiku lililonse angamavutike ndi ululu wamumtima. Ndiye kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji?

  • M’Baibulo muli mfundo zambiri zabwino zimene zingakuthandizeni kuthana ndi maganizo olakwika. (Afilipi 4:8) Kuganizira kwambiri mfundo zimenezi, kungakutonthozeni komanso kungakuthandizeni kukhala odekha ndipo zimenezi zingachititse kuti muziganiza bwino.​—Salimo 94:18, 19.

  • Baibulo lingatithandize kuthana ndi maganizo odziona kuti ndife osafunika.​—Luka 12:6, 7.

  • Malemba osiyanasiyana a m’Baibulo, amatitsimikizira kuti sitili tokha ndipo Mulungu yemwe ndi Mlengi wathu, amamvetsa bwino mmene timamvera mumtima mwathu.​—Salimo 34:18; 1 Yohane 3:19, 20.

  • Baibulo limatilonjeza kuti Mulungu adzathetsa zopweteka za mtundu wina uliwonse ndipo sitidzazikumbukiranso. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4) Lonjezo limeneli limatipatsa mphamvu kuti tipitirizebe kupirira tikamasokonezeka maganizo.

Mmene Baibulo Likumuthandizira Jessica

Mmene Kuvutika Maganizo Kumandikhudzira

Jessica wagona ali ndi Baibulo lotsegula m’manja.

“Ndili ndi zaka 25, ndinadwala kwambiri ndipo atandiyeza anandipeza ndi matenda aakulu ovutika maganizo. Ndinkavutika kwambiri ndi zinthu zoipa zimene zinandichitikira kalekale chifukwa zinkandibwerera mwadzidzidzi m’maganizo mwanga ndipo ndinkalephera kudziletsa. Adokotala anandithandiza kumvetsa kuti vutoli linayamba chifukwa choti ndinkaganizira kwambiri zinthu zoipa zimene zinandichitikira kalekale. Kuwonjezera pa thandizo la mankhwala, ndinkafunikiranso malangizo akuchipatala amene akanandithandiza kuzindikira zimene ndiyenera kuchita kuti ndisinthe kaganizidwe kanga.”

Mmene Baibulo Limandithandizira

“Ndikapanikizika ndi maganizo ndimavutika kwambiri ndi nkhawa komanso ndimalephera kugona. Nthawi zambiri usiku, ndimasowa mtendere wam’maganizo ndipo ndimalephera kudziletsa kuti ndisiye kuganizira zinthu zimene zikundidetsa nkhawazo. Monga mmene lemba la Salimo 94:19 limanenera, Mulungu akhoza kutitonthoza ngati tathedwa nzeru chifukwa cha nkhawa. Choncho ndinaika Baibulo komanso kope limene ndimalembamo mavesi olimbikitsa pafupi ndi bedi langa. Ndiye ndikamalephera kugona usiku, ndimawerenga mavesi amenewo zomwe zili ngati kulola Mulungu kuti andilimbikitse.”

“Baibulo limatilimbikitsa kuti tisinthe maganizo athu amene ali osemphana ndi mfundo zimene timadziwa zokhudza Mulungu. M’mbuyomu, ndinkakhulupirira kuti ndine wachabechabe komanso kuti anthu sangandikonde. Koma ndinaphunzira kuti zimene ndinkakhulupirirazo ndi zosemphana ndi zimene Baibulo limanena. Chifukwa Baibulo limati Mulungu ndi wachikondi komanso Tate wachifundo amene amasamala za aliyense payekha. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuyesetsa kuti ndizitha kulamulira maganizo anga m’malo moti maganizo angawo azindilamulira. Ndinayamba kudziona ngati mmene Mulungu amandionera. Imeneyi inali njira imene inandithandiza kwambiri kuti ndiyambe kudziona moyenera.”

“Ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene kupweteka kwa mtundu wina uliwonse komanso kuvutika maganizo kulikonse kudzatheretu. Kudziwa kuti vuto la matenda amaganizo idzakhala mbiri yakale, kumandipatsa mphamvu kuti ndithe kupirira panopa komanso kumandipatsa chiyembekezo chabwino kuti m’tsogolo, vuto langa la matenda amaganizo lidzatheratu.”

Kuti Mudziwe Zambiri:

Werengani nkhani yakuti, “‘Mulungu Wachitonthozo Chonse’ Amathandiza,” mu Galamukani ya July 2009, pa jw.org/ny.

Mvetserani mawu ochita kujambulidwa a buku la Masalimo pa jw.org, m’Baibulo lachingelezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena