Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp23 No. 1 tsamba 10-11
  • 3 | Zitsanzo za M’Baibulo Zingakuthandizeni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 3 | Zitsanzo za M’Baibulo Zingakuthandizeni
  • sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tanthauzo Lake
  • Mmene Zimenezi Zingakuthandizireni
  • Kukhala ndi Matenda a Maganizo
    Galamukani!—2004
  • Mmene Ena Angathandizire
    Galamukani!—2004
  • Nkhani Yabwino kwa Odwala Matendaŵa
    Galamukani!—2004
  • 2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’
    sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
Onani Zambiri
sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
wp23 No. 1 tsamba 10-11
Mneneri Mose ali ndi nkhawa, wayang’ana kumwamba ndipo akupemphera kwa Mulungu.

3 | Zitsanzo za M’Baibulo Zingakuthandizeni

BAIBULO LIMAFOTOKOZA ZA . . . Amuna ndi akazi okhulupirika amene anavutikapo ndi nkhawa ndipo anali ‘anthu ngati ife tomwe.’​—YAKOBO 5:17.

Tanthauzo Lake

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zimene zinachitikadi za amuna ndi akazi amene anavutikapo ndi nkhawa zosiyanasiyana. Tikamawerenga nkhani zimenezi, tikhoza kupeza zitsanzo zimene zingafanane ndi zimene zikutichitikira ifeyo.

Mmene Zimenezi Zingakuthandizireni

Tonsefe timafuna titadziwa ngati anthu ena amamvetsa mmene timamvera, makamaka ngati tikuvutika ndi matenda amaganizo. Tikamawerenga Baibulo, timaphunzira za anthu amene ankaganiza komanso kumva ngati mmene ifeyo timamvera. Zimenezi zimatithandiza kuzindikira kuti pali anthu enanso amene anakumanapo ndi mavuto a nkhawa komanso kuvutika maganizo ndipo timamva kuti sitili tokha.

  • M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anadzimvapo kuti ndi osafunika ndipo alibe chiyembekezo chilichonse. Kodi munayamba mwavutikapo maganizo mpaka kufika ponena kuti, ‘Basi ine ndatopa nazo?’ Mose, Eliya komanso Davide anamvapo choncho.​—Numeri 11:14; 1 Mafumu 19:4; Salimo 55:4.

  • Baibulo limatiuza za mzimayi wina dzina lake Hana amene ‘anakhumudwa kwambiri’ chifukwa choti anali wosabereka ndiponso mkazi mnzake ankamunyoza kwambiri.​—1 Samueli 1:6, 10.

  • Baibulo limatiuzanso za munthu wina dzina lake Yobu yemwe chitsanzo chake chingatithandizenso. Ngakhale kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova, iye anavutikapo ndi nkhawa mpaka kufika ponena kuti: “Moyo ndaukana sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”​—Yobu 7:16.

Ifenso tikhoza kupeza mphamvu zimene zingatithandize kulimbana ndi nkhawa zosiyanasiyana, tikamaganizira zitsanzo za anthu ngati amenewa omwe anakwanitsa kulimbana ndi maganizo olakwika.

Mmene Baibulo Likumuthandizira Kevin

Mmene Matenda Ovutika Maganizo Amandikhudzira

Kevin akumwa khofi ndi anzake.

“Nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 50, ndinapezeka ndi matenda amaganizo (bipolar disorder) amene amachititsa munthu kusinthasintha zochita. Nthawi zina, ndimamva kuti ndikhoza kulimbana ndi vuto lililonse limene ndikukumana nalo pa moyo wanga. Koma nthawi zina ndimamvanso kuti kuli bwino ndingofa basi.”

Mmene Baibulo Limandithandizira

“Chitsanzo cha m’Baibulo chimene chimandithandiza ndi cha mtumwi Petulo. Iye analakwitsapo zinthu zina zimene zinamupangitsa kuti adziziona kuti ndi wosafunika. Koma m’malo momangoganizira zimenezi, mtumwi Petulo anayesetsa kupeza anzake amene angamuthandize. Nthawi zina ndikakhala kuti ndikuvutika kwambiri ndi matenda amaganizo, ndimayamba kudziona kuti ndine munthu wosafunika chifukwa cha zinthu zimene ndimalakwitsa. Ndiye potengera mtumwi Petulo, nanenso ndimayesetsa kuti ndizicheza ndi anzanga amene angandithandize kuti ndisafooke.”

“Chitsanzo chinanso cha m’Baibulo chimene chimandilimbikitsa kwambiri ndi cha Mfumu Davide. Nthawi zambiri ankakhumudwa ndipo ankanong’oneza bondo chifukwa cha zinthu zimene analakwitsa kalekale. Inenso ndimamva ngati Mfumu Davide chifukwa nthawi zina ndimalankhula kapena kuchita zinthu zimene ndimadzanong’oneza nazo bondo. Zimene Davide analankhula pa Salimo 51 zimandilimbikitsa. Pa vesi 3 ananena kuti: “Zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.” Zimenezi ndi zimene zimandichitikira ndikavutika kwambiri ndi maganizo chifukwa ndimalephera kuganizira zinthu zabwino zokhudza ineyo. Koma ndimalimbikitsidwanso ndikaganizira zimene ananena pa vesi 10, pomwe anati: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” Inenso ndimachita chimodzimodzi pomupempha Mulungu kuti andithandize kuti ndidziziona moyenera. Pomaliza ndimalimbikitsidwanso ndi zimene vesi 17 limanena, lomwe limati: ‘Mulungu, sadzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.’ Vesi limeneli, limanditsimikizira kuti Mulungu amandikondadi.”

“Kuganizira kwambiri zitsanzo za m’Baibulo komanso zimene Mulungu wandipatsa panopa, zimalimbitsa chiyembekezo changa cha m’tsogolo. Ndimaona kuti malonjezo a m’Baibulo ndi enieni ndipo zimenezi zimandithandiza kupitirizabe kupirira.”

Kuti Mudziwe Zambiri:

Werengani nkhani yakuti, “Kukhala ndi Matenda a Maganizo” mu Galamukani ya January 8, 2004, pa jw.org/ny.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena