Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w24 August tsamba 8-13
  • Yehova Amafuna Kuti Anthu Onse Alape

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amafuna Kuti Anthu Onse Alape
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE YEHOVA ANAPHUNZITSA AISIRAELI PA NKHANI YOKHUDZA KULAPA
  • MMENE YEHOVA AMATHANDIZIRA ANTHU OCHIMWA KUTI ALAPE
  • ZIMENE OTSATIRA A YESU ANAPHUNZIRA ZOKHUDZA KULAPA
  • Zimene Yehova Wachita Kuti Atipulumutse ku Uchimo ndi Imfa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Mmene Tingasonyezere Chikondi ndi Chifundo Wina Akachita Tchimo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Akulu Angathandize Bwanji Anthu Amene Achotsedwa Mumpingo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Mpingo Ungatsanzire Bwanji Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Anthu Ochimwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24 August tsamba 8-13

NKHANI YOPHUNZIRA 32

NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika

Yehova Amafuna Kuti Anthu Onse Alape

“Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”​—2 PET. 3:9.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona zimene kulapa kumatanthauza, chifukwa chake kuli kofunika komanso mmene Yehova wakhala akuthandizira anthu onse kuti alape.

1. Kodi kulapa kumatanthauza chiyani?

TIKACHITA chinachake choipa, pamafunika kuti tilape. Baibulo limati munthu amene walapa amayamba kudana ndi zoipa zimene wachitazo, amasiya kuzichita komanso amatsimikiza mtima kuti asazichitenso.​—Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Kulapa.”

2. N’chifukwa chiyani tonsefe timafunika kuphunzira zokhudza kulapa? (Nehemiya 8:9-11)

2 Munthu aliyense ayenera kuphunzira zokhudza kulapa. Chifukwa chiyani? Chifukwa tonsefe timachimwa tsiku lililonse. Monga ana a Adamu ndi Hava, tonse tinatengera uchimo ndi imfa. (Aroma 3:23; 5:12) Palibe ngakhale mmodzi amene ndi wosachimwa. Ngakhale anthu omwe anali ndi chikhulupiriro cholimba ngati mtumwi Paulo ankalimbananso ndi uchimo. (Aroma 7:21-24) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti nthawi zonse tizingokhala okhumudwa chifukwa cha machimo athu? Ayi, Yehova ndi wachifundo ndipo amafuna kuti tizisangalala. Taganizirani zimene zinachitikira Ayuda a m’nthawi ya Nehemiya. (Werengani Nehemiya 8:9-11.) Yehova sankafuna kuti iwo azidzimvera chisoni chifukwa cha machimo omwe anachita kale koma ankafuna kuti azimulambira mosangalala. Yehova amadziwa kuti tikalapa timasangalala. Choncho amatiphunzitsa zokhudza kulapa. Tikalapa machimo athu, tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wachifundo atikhululukira.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi tikambirana mbali zitatu zokhudza kulapa. Choyamba, tiona zimene Yehova anaphunzitsa Aisiraeli zokhudza nkhaniyi. Kenako tiona mmene iye wakhala akuthandizira anthu ochimwa kuti alape. Pomaliza tikambirana zimene Yesu anaphunzitsa otsatira ake zokhudza kulapa.

ZIMENE YEHOVA ANAPHUNZITSA AISIRAELI PA NKHANI YOKHUDZA KULAPA

4. Kodi Yehova anaphunzitsa chiyani Aisiraeli pa nkhani yokhudza kulapa?

4 Yehova atasankha Aisiraeli kuti akhale mtundu wake, anachita nawo pangano ndipo iwo analonjeza kuti azimumvera. Akamamvera malamulo ake, iye ankawateteza komanso kuwadalitsa. Ponena za malamulowo, Yehova ananena kuti: “Lamulo limene ndikukupatsani leroli si lovuta kwa inu kulitsatira, ndipo silili poti simungathe kulipeza.” (Deut. 30:11, 16) Koma akapanda kumumvera, mwina posankha kulambira milungu ina, iye ankasiya kuwadalitsa ndipo ankakumana ndi mavuto. Ngakhale zinali choncho, zinali zotheka kuti Mulungu ayambirenso kuwakonda. Iwo akanatha ‘kubwerera kwa Yehova Mulungu wawo komanso kumvera mawu ake.’ (Deut. 30:1-3, 17-20) M’mawu ena tingati iwo akanatha kulapa. Ndipo Yehova akanatha kukhalanso nawo pa ubwenzi n’kuyambiranso kuwadalitsa.

5. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti sanawasiye anthu ake? (2 Mafumu 17:13, 14)

5 Anthu a Yehova ankamuchimwira mobwerezabwereza. Kuwonjezera pa kulambira mafano, iwo ankachitanso makhalidwe ena oipa. Izi zinachititsa kuti azikumana ndi mavuto. Koma Yehova sanatope nawo anthu ake osamverawa. Mobwerezabwereza, ankawatumizira aneneri n’cholinga choti alape ndi kubwerera kwa iye.​—Werengani 2 Mafumu 17:13, 14.

6. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji aneneri pophunzitsa anthu ake kufunika kolapa? (Onaninso chithunzi.)

6 Nthawi zonse Yehova ankagwiritsa ntchito aneneri pofuna kuchenjeza komanso kuthandiza anthu ake kuti asinthe. Mwachitsanzo, kudzera mwa Yeremiya, Mulungu ananena kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya chifukwa ndine wokhulupirika . . . Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. Koma vomerezani kuti ndinu olakwa chifukwa mwapandukira Yehova.” (Yer. 3:12, 13) Kudzera mwa Yoweli, Yehova anati: “Bwererani kwa ine ndi mtima wonse.” (Yow. 2:12, 13) Anauzanso Yesaya kuti alengeze kuti: “Dziyeretseni. Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kuchita zoipa.” (Yes. 1:16-19) Ndiponso kudzera mwa Ezekieli, Yehova anafunsa kuti: “Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wochimwa? Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wochimwayo alape nʼkupitiriza kukhala ndi moyo? Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense, . . choncho siyani kuchita zoipa kuti mupitirize kukhala ndi moyo.” (Ezek. 18:23, 32) Yehova amasangalala akaona kuti anthu alapa chifukwa iye amafuna kuti iwo apitirize kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Choncho Yehova samangokhala n’kumayembekezera kuti anthu ochimwawo asinthe, popanda kuwathandiza. Tiyeni tione zitsanzo pa nkhaniyi.

Zithunzi: Aneneri amene Yehova anawatumiza kuti akathandize anthu ake osamvera. 1. Yoweli: cha m’ma 820 B.C.E. 2. Hoseya: pambuyo pa 745 B.C.E. 3. Yesaya: pambuyo pa 732 B.C.E. 4. Ezekieli: cha m’ma 591 B.C.E. 5. Yeremiya: 580 B.C.E.

Nthawi zambiri Yehova ankatumiza aneneri kuti akalimbikitse anthu ake osamvera kuti alape (Onani ndime 6-7)


7. Pogwiritsa ntchito nkhani ya mneneri Hoseya ndi mkazi wake, kodi Yehova anaphunzitsa chiyani anthu ake?

7 Onani zimene Yehova anaphunzitsa anthu ake pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mneneri Hoseya ndi mkazi wake Gomeri. Gomeri anachita chigololo ndipo anasiya Hoseya n’kupita kwa mwamuna wina. Kodi Mulungu anamuona kuti iye sangasinthe? Yehova yemwe amatha kudziwa zomwe zili mumtima mwa munthu anauza Hoseya kuti: “Pita ukayambenso kukonda mkazi amene akukondedwa ndi mwamuna wina ndipo akuchita chigololo. Ukamukonde ngati mmene Yehova amakondera Aisiraeli, ngakhale kuti iwo amalambira milungu ina.” (Hos. 3:1; Miy. 16:2) Dziwani kuti mkazi wa Hoseya anali asanasiye kuchita tchimo lalikululi. Koma Yehova anauza Hoseya kuti apite kwa mkaziyo, kumukhululukira ndi kumutenganso monga mkazi wake.a Mofanana ndi zimenezi, Yehova sanasiye kukonda anthu ake omwe anali osamvera. Ngakhale kuti iwo ankachita machimo akuluakulu, iye ankawakondabe komanso anapitiriza kuwathandiza kuti alape n’kusintha zochita zawo. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova yemwe amadziwa za mumtima angathandizebe munthu yemwe akupitiriza kuchita tchimo lalikulu kuti alape? (Miy. 17:3) Tiyeni tione.

MMENE YEHOVA AMATHANDIZIRA ANTHU OCHIMWA KUTI ALAPE

8. Kodi Yehova anatani pofuna kuthandiza Kaini kuti alape? (Genesis 4:3-7) (Onaninso chithunzi.)

8 Kaini anali mwana woyamba wa Adamu ndi Hava. Iye anatengera uchimo kuchokera kwa makolo akewa. Ponena za iye Baibulo limanenanso kuti: “Zochita zake zinali zoipa.” (1 Yoh. 3:12) Mwina n’chifukwa chake Yehova “sanasangalale ndi Kaini komanso nsembe yake ngakhale pangʼono.” M’malo mosintha zochita zake, “Kaini anapsa mtima kwambiri ndipo nkhope yake inagwa chifukwa cha chisoni.” Ndiye kodi kenako Yehova anachita chiyani? Iye analankhula ndi Kaini. (Werengani Genesis 4:3-7.) Onani kuti Yehova analankhula ndi Kaini mokoma mtima, anamuuza kuti adzamudalitsa ngati atachita zabwino komanso anamuchenjeza za kuopsa kwa tchimo. N’zomvetsa chisoni kuti Kaini sanamvere. Iye sanalole kuti Yehova amuthandize kuti alape. Koma kodi Kaini atakana kumvera, Yehova anasiya kuthandiza anthu ena ochimwa kuti alape? Ayi sanatero.

Kaini watenga mtengo ndipo akupita kukapha Abele. Kenako akutembenuka kuti amve zimene Yehova akulankhula kuchokera kumwamba.

Yehova analankhula ndi Kaini mokoma mtima, n’kumuuza kuti akhoza kumudalitsa ngati atasintha komanso anamuchenjeza za kuopsa kwa tchimo (Onani ndime 8)


9. Kodi Yehova anathandiza bwanji Davide kuti alape?

9 Yehova ankakonda kwambiri Mfumu Davide. Iye anafika pomutchula kuti “munthu wapamtima panga.” (Mac. 13:22) Koma Davide anachita machimo akuluakulu monga chigololo komanso kupha munthu. Malinga ndi Chilamulo cha Mose, Davide ankayenera kuphedwa. (Lev. 20:10; Num. 35:31) Koma mokoma mtima Yehova anamuthandiza kuti alape.b Iye anamutumizira mneneri wake Natani ngakhale kuti Davide anali asanasonyeze kulapa kulikonse. Natani anagwiritsa ntchito fanizo limene linamufika pamtima Davide. Atazindikira kuti wakhumudwitsa Yehova, Davide analapa. (2 Sam. 12:1-14) Pambuyo pake analemba salimo losonyeza kudzimvera chisoni ndi zomwe anachita. (Sal. 51, timawu tapamwamba) Salimoli lakhala likutonthoza anthu ambiri ochimwa komanso kuwalimbikitsa kuti alape. Timayamikira kwambiri kuti Yehova anathandiza mtumiki wake wokondedwa Davide kuti alape.

10. Kodi mumamva bwanji mukaganizira za kuleza mtima komanso kukhululuka kwa Yehova akamachita zinthu ndi anthu ochimwa?

10 Yehova amadana ndi tchimo lamtundu uliwonse. (Sal. 5:4, 5) Komabe iye amadziwa kuti tonsefe ndi ochimwa ndipo chifukwa chakuti amatikonda, amafuna kutithandiza kulimbana ndi uchimowo. Nthawi zonse amafunitsitsa kuthandiza ngakhale anthu ochimwa kwambiri kuti alape n’kukhalanso naye pa ubwenzi. Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri. Tikamaganizira kuleza mtima komanso kukhululuka kwa Yehova, timafunitsitsa kukhalabe okhulupirika kwa iye ndiponso kulapa mwamsanga tikachimwa. Tsopano tiyeni tione mmene Yesu anathandizira ophunzira ake kudziwa zambiri pa nkhani yokhudza kulapa.

ZIMENE OTSATIRA A YESU ANAPHUNZIRA ZOKHUDZA KULAPA

11-12. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito fanizo liti pofuna kutithandiza kudziwa kuti Atate wake ndi wokonzeka kutikhululukira? (Onani chithunzi chapachikuto.)

11 Tsopano nthawi inafika pomwe Mesiya anaonekera. Monga tinaonera munkhani yapita ija, Yehova anagwiritsa ntchito Yohane M’batizi komanso Yesu Khristu pophunzitsa anthu kufunika kolapa.​—Mat. 3:1, 2; 4:17.

12 Ali padziko lapansi Yesu anaphunzitsa anthu kuti Atate wake ndi wokonzeka kutikhululukira tikachimwa. Yesu anachita zimenezi pofotokoza fanizo la mwana wolowerera. Mwanayo anasankha kuchoka pakhomo pa makolo ake n’kumakachita zoipa. Koma pambuyo pake “nzeru zitamubwerera,” anabwerera kwawo. Ndiye kodi bambo ake anatani? Yesu ananena kuti mwanayo “ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa ndi chifundo. Kenako anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa mwachikondi.” Mwanayo anapempha bambo akewo kuti amutenge ngati wantchito wawo, koma bambowo anamutchula kuti “mwana wangayu,” kusonyeza kuti ankamuonabe kuti ndi mwana wawo. Bambowo anati: “Anatayika koma wapezeka.” (Luka 15:11-32) Mosakayikira Yesu asanabwere padzikoli, ankaona Atate wake akusonyeza chifundo kwa anthu olapa ambirimbiri. Fanizo la Yesuli limatilimbikitsa ndipo limatitsimikizira kuti Atate wathu Yehova ndi wachifundo.

Mwana wolowerera wa mu fanizo la Yesu akuwerama pamaso pa bambo ake omwe akuthamanga kuti adzamuhage.

Bambo wa mufanizo la Yesu la mwana wolowerera akuthamanga ndi kuhaga mwana wake yemwe wabwerera kunyumba (Onani ndime 11-12)


13-14. Kodi mtumwi Petulo anaphunzira chiyani zokhudza kulapa, nanga anaphunzitsa ena zotani pa nkhaniyi? (Onaninso chithunzi.)

13 Mtumwi Petulo anaphunzira mfundo zofunika kuchokera kwa Yesu pa nkhani yokhudza kulapa ndi kukhululuka. Nthawi zambiri Petulo ankalakwitsa zinthu ndipo Yesu ankamukhululukira. Mwachitsanzo, iye atakana Mbuye wake maulendo atatu, anakhumudwa kwambiri. (Mat. 26:34, 35, 69-75) Koma Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa Petulo mwina pa nthawi imene anali payekha. (Luka 24:33, 34; 1 Akor. 15:3-5) Mosakayikira pa nthawiyi, Yesu anamutsimikizira mwachikondi mtumwi wake wolapayu kuti anamukhululukira.​—Maliko 16:7.

14 Popeza ankadziwa mmene munthu amamvera akalapa n’kukhululukidwa, Petulo akanatha kuphunzitsa ena zokhudza nkhanizi. Pa nthawi ina pambuyo pa Chikondwerero cha Pentekosite, Petulo anakambira nkhani gulu la Ayuda yofotokoza kuti iwo anapha Mesiya. Koma mwachikondi iye anawalimbikitsa kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwere kuchokera kwa Yehova.” (Mac. 3:14, 15, 17, 19) Apa Petulo anasonyeza kuti kulapa kumamuthandiza munthu wochimwa kuti atembenuke, kutanthauza kuti asiye zoipa zimene amaganiza kapena kuchita, n’kuyamba kuchita zabwino zimene zingasangalatse Mulungu. Mtumwiyu anasonyezanso kuti Yehova amakhululuka kotheratu, zomwe zimakhala ngati wafufuta machimowo. Patapita zaka zambiri, Petulo anatsimikizira Akhristu kuti: “Yehova . . . akukulezerani mtima chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) N’zolimbikitsatu kudziwa kuti tikalapa machimo athu ngakhale atakhala akuluakulu, Yehova amatikhululukira.

Zithunzi: 1. Mtumwi Petulo akulira mopwetekedwa mtima. 2. Yesu waukitsidwa ndipo akulankhula ndi Petulo molimbikitsa.

Yesu anasonyeza chikondi pokhululukira mtumwi wake yemwe analapa ndipo anamulimbikitsa (Onani ndime 13-14)


15-16. (a) Kodi Paulo anaphunzira bwanji zokhudza kukhululuka? (1 Timoteyo 1:12-15) (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

15 Saulo wa ku Tariso anachita zoipa zambiri ndipo ankafunika kulapa kuti akhululukidwe. Iye ankazunza mwankhaza otsatira a Khristu. Akhristu ambiri ayenera ankaganiza kuti iye sangalape n’kusintha. Koma Yesu ankadziwa kuti Saulo akhoza kusintha. Iye ndi Atate wake ankaona makhalidwe abwino omwe Saulo anali nawo. Yesu anati: “Munthu ameneyu ndi chiwiya changa chosankhidwa.” (Mac. 9:15) Yesu anafika pochita zodabwitsa pofuna kuthandiza Saulo kuti alape. (Mac. 7:58–8:3; 9:1-9, 17-20) Atakhala Mkhristu, nthawi zambiri Saulo, yemwe pambuyo pake ankadziwika kuti mtumwi Paulo, ankayamikira mmene Yehova ndi Yesu anamusonyezera chifundo ndi kukoma mtima. (Werengani 1 Timoteyo 1:12-15.) Mtumwiyu ananena kuti: “Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, . . . nʼcholinga choti ulape.”​—Aroma 2:4.

16 Kodi Paulo anachita chiyani atamva za tchimo lina lachigololo lomwe linachitika mumpingo wa ku Korinto? Iye anasamalira nkhaniyi m’njira imene imatiphunzitsa kufunika kosonyeza chifundo komanso kuti Yehova amatilangiza mwachikondi tikachimwa. Tikambirana zambiri pa nkhaniyi munkhani yotsatira.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yehova anaphunzitsa chiyani Aisiraeli pa nkhani ya kulapa?

  • Kodi Yehova wakhala akuthandiza bwanji anthu ochimwa kuti alape?

  • Kodi otsatira a Yesu anaphunzira chiyani pa nkhani yokhudza kulapa?

NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako

a Nkhani ya Hoseyayi ndi yapadera chifukwa masiku ano Yehova sanaike lamulo lakuti munthu akachita chigololo, mnzake wosalakwayo apitirizebe kukhala naye pa banja. Ndipotu Yehova anauza Mwana wake kuti afotokoze kuti wolakwiridwayo angathe kukatenga chikalata chothetsera ukwati ngati akufuna kutero.​—Mat. 5:32; 19:9.

b Onani nkhani yakuti “Yehova Ndi Wofunitsitsa Kukukhululukirani” mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2012, tsamba 21-23, ndime 3-10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena