Kodi Anthu Angathetse Nkhondo Komanso Zachiwawa?
Nkhondo imayambika pazifukwa zosiyanasiyana. Anthu ena amamenyana pazifukwa za ndale, zachuma komanso pofuna kumenyera maufulu awo. Pomwe ena amamenyana polimbirana malo kapena zinthu zina zofunikira za m’chilengedwe. Nkhondo zambiri zimayamba chifukwa chosiyana mitundu komanso zipembedzo. Kodi anthu akuchita zotani kuti athetse nkhondo ndi kukhazikitsa mtendere? Kodi zimene anthu akuyesa kuchita zingathandizedi kuti nkhondo zithe?
Drazen_/E+ via Getty Images
KUPITITSA PATSOGOLO NKHANI ZA CHUMA
Cholinga chawo: Kuthandiza anthu kuti zinthu ziziwayendera bwino pa nkhani za chuma. Zimenezi zingathandize kuthetsa kapena kuchepetsa umphawi, womwe nthawi zambiri umayambitsa mikangano.
N’chifukwa chiyani zili zovuta? Maboma afunika kusintha mmene amagwiritsira ntchito ndalama. Mu 2022, ndalama zokwana madola a ku America pafupifupi 34.1 biliyoni zinagwiritsidwa ntchito pofuna kukhazikitsa mtendere padziko lonse. Komabe, zimenezi ndi ndalama zochepa kwambiri poyerekezera ndi zomwe zinagwiritsidwa ntchito pa zinthu zokhudza nkhondo chaka chomwecho.
“Timawononga ndalama komanso chuma chambiri pothandiza anthu amene akhudzidwa ndi nkhondo m’malo mogwiritsa ntchito ndalamazo popewa nkhondo ndi kulimbikitsa mtendere.”—António Guterres, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations.
Zimene Baibulo limanena: Maboma komanso mabungwe a m’dzikoli akhoza kuyesetsa kuthandiza anthu osauka koma sangathetseretu umphawi.—Deuteronomo 15:11; Mateyu 26:11.
KUGWIRIZANA ZOLIMBIKITSA MTENDERE
Cholinga chawo: Kupewa kapenanso kuthetsa mikangano mwamtendere pokambirana njira zothetsera mavuto m’njira zokomera mbali zonse.
N’chifukwa chiyani zili zovuta? Gulu limodzi kapena magulu angapo sangafune kukambirana, kulolera kapenanso kuvomereza mgwirizano. Komanso anthu amaphwanya mfundo za mgwirizano wa mtendere mosavuta.
“Si nthawi zonse pamene mgwirizano wolimbikitsa mtendere umayenda bwino. Mgwirizano wofuna kuthetsa nkhondo ukhoza kukhala ndi mavuto ndipo ungachititse kuti mkangano uzingowonjezereka.”—Raymond F. Smith, American Diplomacy.
Zimene Baibulo limanena: Anthu ayenera “kukhala mwamtendere.” (Salimo 34:14) Koma anthu ambiri masiku ano ndi “osakhulupirika, . . . osafuna kugwirizana ndi ena, . . . ochitira anzawo zoipa.” (2 Timoteyo 3:1-4) Makhalidwe amenewa amachititsa kuti atsogoleri andale ena amaganizo abwino alephere kuthetsa mikangano.
KUGWIRIZANA ZOTHETSA KAPENA KUCHEPETSA ZIDA ZANKHONDO
Cholinga chawo: Kuchepetsa kapena kuthetseratu zida zankhondo, makamaka zanyukiliya, za poizoni komanso zofalitsa tizilombo toyambitsa matenda.
N’chifukwa chiyani zili zovuta? Mayiko safuna kuwononga zida zimenezi chifukwa amaopa kuti mphamvu zawo zichepa ndipo sangathe kudziteteza. Ndipotu kuwononga zida sikungathetse vuto limene limachititsa kuti anthu azimenyana.
“Maboma ambiri amene analonjeza kuti awononga zida zawo pambuyo pa chaka cha 1991, sanachite zimene analonjezazo monga kuchepetsa zinthu zoyambitsa nkhondo komanso mikangano ya mayiko, moti akanachita zimenezi bwenzi anthufe tikukhala m’dziko lamtendere ndiponso lotetezeka kwambiri.”—“Securing Our Common Future: An Agenda for Disarmament.”
Zimene Baibulo limanena: Anthu ayenera kutaya zida za nkhondo ndiponso ‘kusula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo.’ (Yesaya 2:4) Komabe, kuti nkhondo zithe, anthu akufunika kuchita zambiri kuposa pamenepa chifukwa zachiwawa zimayambira mumtima.—Mateyu 15:19.
KUPANGA MGWIRIZANO WOFUNA KUPEWA NKHONDO
Cholinga chawo: Maboma amapanga mgwirizano woti azitetezana kwa adani. Iwo amaganiza kuti palibe dziko lomwe lingayambitse nkhondo ndi dziko lililonse limene lili mumgwirizano wawo chifukwa likhala likulimbana ndi mayiko onse mumgwirizanowo.
N’chifukwa chiyani zili zovuta? Kukhala mumgwirizano woti mayiko azitetezana sikungalepheretse nkhondo. Kawirikawiri mayiko omwe apanga mgwirizano sakwaniritsa zomwe analonjeza komanso sagwirizana pa njira zina zodzitetezera ndiponso nthawi yomwe angathe kulimbana ndi adani.
“Ngakhale kuti mabungwe a League of Nations ndi United Nations anayesetsa kuthandiza maboma kuti apange mgwirizano wotetezana, migwirizano imeneyi sinathandize kuti nkhondo zithe.”—“Encyclopedia Britannica.”
Zimene Baibulo limanena: Nthawi zambiri zinthu zimayenda bwino ngati anthu akuchitira zinthu limodzi. (Mlaliki 4:12) Komabe, sitingadalire maboma kapena mabungwe a anthu kuti abweretse mtendere padzikoli. Baibulo limanena kuti: “Musamakhulupirire anthu olemekezeka kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso. Mpweya wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.”—Salimo 146:3, 4.
Ngakhale kuti mayiko akuyesetsa kuti padzikoli pakhale mtendere, anthu akuvutikabe ndi nkhondo.